Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

June 30–July 6

MIYAMBO 20

June 30–July 6

Nyimbo Na. 131 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Mfundo Zothandiza Kuti Chibwenzi Chanu Chiyende Bwino

(10 min.)

Muziganizira mmene Yehova amaonera zibwenzi (Miy 20:24, 25; w24.05 26-27 ¶3-4)

Muziyesetsa kuti mumudziwe munthu amene mukumufunayo musanayambe chibwenzi (Miy 20:18; w24.05 22 ¶8)

Muzidziwana bwino pa nthawi imene muli pachibwenzi (Miy 20:5; w24.05 28 ¶7-8)

KUMBUKIRANI: Anthu akhoza kusankha kuti asakwatirane koma athetse chibwenzicho, ndipo zikatero zimakhalabe kuti chibwenzicho chayenda bwino.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Miy 20:27—Kodi “mpweya wa munthu ndi nyale ya Yehova” m’njira yotani? (it-2 196 ¶7)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo wakuuzani kuti wasamukira kumene kwanuko kuchokera ku dziko lina. (lmd phunziro 3 mfundo 3)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Muuzeni za JW Library® ndipo musonyezeni mmene angaiikire muchipangizo chake. (lmd phunziro 9 mfundo 5)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(4 min.) Chitsanzo. ijwbq nkhani na. 159—Mutu: Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba? (lmd phunziro 3 mfundo 4)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 78

7. Muzilimbikitsa Anthu kuti Ayambe Kuphunzira Baibulo

(5 min.) Nkhani yokambirana.

Kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi mbali yofunika kwambiri ya utumiki wathu. Ndiye zingatheke bwanji kuthandiza ena kukhala ophunzira a Khristu ngati sitiphunzira nawo Baibulo? (Aro 10:13-15) Mwina mungakhale ndi cholinga choti muziyambitsa phunziro la Baibulo mwachindunji pamene mukulalikira khomo ndi khomo. Kuti zimenezi zitheke, ganizirani nkhani imene mwininyumba angachite nayo chidwi. Kenako, musonyezeni mmene kuphunzira Baibulo kungamuthandizire pa moyo wake komanso mmene kungamuthandizire kupeza mayankho a mafunso amene ali nawo.

Pa jw.org pali linki yakuti “Yambani Kuphunzira Baibulo” yomwe ingakuthandizeni kuuza anthu omwe mwakumana nawo za phunziro la Baibulo.

  • Kodi linki yakuti “Yambani Kuphunzira Baibulo” mungaigwiritse ntchito bwanji poyambitsa phunziro la Baibulo?

  • Kodi ndi njira ziti zimene kwanuko mumaona kuti ndi zothandiza kwambiri poyambitsa maphunziro a Baibulo?

8. Vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya June

(10 min.) Onerani VIDIYOYI.

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 28 ¶8-15

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 150 ndi Pemphero