KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI
Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo
Tikamapanga maulendo obwereza kapena kuchititsa maphunziro a Baibulo, tiyenera kuthandiza amene tikuwaphunzitsawo kumvetsa mfundo zikuluzikulu. Tikamagwiritsa ntchito mafanizo pofotokoza mfundozi, timawafika pamtima komanso amazikumbukira mosavuta.
Mukamakonzekera ulendo wobwereza kapena phunziro la Baibulo, muzisankha mfundo zikuluzikulu, osati zing’onozing’ono, zomwe mukagwiritse ntchito mafanizo pozifotokoza. Kenako pezani mafanizo osavuta kumva omwe ndi ogwirizana ndi moyo wa tsiku ndi tsiku. (Mt 5:14-16; Mko 2:21; Lu 14:7-11) Mukamakonzekera, muziganizira zokhudza moyo komanso zimene munthuyo amachita. (Lu 5:2-11; Yoh 4:7-15) Mukaona munthuyo akusangalala chifukwa choti wamvetsa bwino mfundo yaikulu, inunso mudzasangalala.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA—MUZIGWIRITSA NTCHITO MAFANIZO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
N’chifukwa chiyani ophunzira amafunika kuwathandiza kuti amvetse bwino mavesi a m’Baibulo?
-
Kodi Anita anagwiritsira ntchito bwanji fanizo pofotokoza mfundo ya pa Aroma 5:12?
-
Mafanizo abwino amafika anthu pamtima
Kodi mafanizo abwino angathandize bwanji omvera athu?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kumagwiritsa ntchito mavidiyo komanso zinthu zina zophunzitsira zimene gulu la Yehova latipatsa tikakhala mu utumiki?