April 29–May 5
MASALIMO 34-35
Nyimbo Na. 10 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Muzitamanda Yehova Nthawi Zonse”
(10 min.)
Davide ankatamanda Yehova ngakhale pamene ankakumana ndi mayesero (Sl 34:1; w07 3/1 22 ¶11)
Davide ankadzitamandira mwa Yehova, osati kudzitamandira yekha (Sl 34:2-4 mawu a m’munsi; w07 3/1 22 ¶13)
Zomwe Davide ankachita potamanda Yehova zinalimbikitsa anzake (Sl 34:5; w07 3/1 23 ¶15)
Davide atapulumuka kwa Abimeleki, amuna ena 400 omwe sankasangalala ndi ulamuliro wa Sauli anamupeza kuchipululu. (1Sa 22:1, 2) Davide ayenera kuti ankaganizira za anthu amenewa pamene ankalemba salimo limeneli.—Sl 34, kamutu.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndidzatamande bwanji Yehova polankhula ndi munthu wina pamisonkhano yampingo yotsatira?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 35:19—Kodi zomwe Davide anapempha zoti Yehova asalole kuti anthu amene amadana naye ‘amupsinyire diso’ zimatanthauza chiyani? (w06 5/15 20 ¶1)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 34:1-22 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Mwasiya kulankhula ndi munthu musanamulalikire. (lmd phunziro 1 mfundo 4)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Chitsanzo. ijwfq 59—Mutu: Kodi a Mboni za Yehova Amadziwa Bwanji Ngati Holide Inayake ndi Yovomerezeka? (th phunziro 17)
Nyimbo Na. 59
7. Njira Zitatu za Mmene Tingatamandire Yehova Pamisonkhano
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Timakhala ndi mwayi waukulu wotamanda Yehova pamisonkhano yampingo. Taonani njira zitatu zotsatirazi:
Kucheza: Mukamacheza ndi anthu ena muzikambirana nawo za ubwino wa Yehova. (Sl 145:1, 7) Kodi mwawerenga kapena kumva mfundo inayake imene yakuthandizani? Kodi pali zinthu zina zabwino zimene zakuchitikirani mu utumiki? Kodi munthu wina wachita kapena kulankhula zinthu zimene zakulimbikitsani? Kodi mwaona zinthu zinazake zachilengedwe zimene zakuchititsani chidwi? Zonsezi ndi mphatso zochokera kwa Yehova. (Yak 1:17) Muzifika pamisonkhano mwamsanga ndi cholinga choti mupeze nthawi yocheza ndi anthu ena.
Kuyankha: Muziyesetsa kuyankhapo ngakhale kamodzi kokha pa msonkhano uliwonse. (Sl 26:12) Mukhoza kupereka yankho lachindunji la funso, kupereka yankho lowonjezera, kufotokozera lemba, chithunzi kapena mmene tingagwiritsire ntchito zomwe tikuphunzirazo. Muzikonzekera mayankho ambiri, chifukwa mwina ena akhoza kuyankhanso pa ndime imene munakonzekera. Anthu ambiri adzakhala ndi mwayi ‘wotamanda Mulungu’ ngati mayankho athu ali osapitirira masekondi 30.—Ahe 13:15.
Nyimbo: Muziimba nyimbo za Ufumu ndi mtima wonse. (Sl 147:1) Nthawi zonse sangakulozeni kuti muyankhe pamene mwaimika dzanja makamaka ngati muli mumpingo waukulu, koma mumakhala ndi mwayi woimba nyimbo. Ngakhale mumaona kuti simutha kuimba, Yehova amasangalala kwambiri mukamaimba ndi mtima wonse. (2Ak 8:12) Mukhoza kumakonzekera poyeserera nyimbozi muli kunyumba.
Onerani VIDIYO yakuti Mbiri ya Gulu Lathu—Mphatso ya Nyimbo, Mbali Yoyamba. Kenako funsani omvera funso ili:
Pamene gulu lathu linkayamba, kodi tinasonyeza bwanji kuti kuimba nyimbo zotamanda Yehova ndi kofunika kwambiri?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 9 ¶1-7, mawu ofotokoza gawo 3 ndi bokosi patsamba 70