Yosefe Anakhululukira Azichimwene Ake
Kukhululuka kumakhala kovuta makamaka ngati munthu watikhumudwitsa mwadala. Kodi n’chiyani chinathandiza Yosefe kukhululukira azichimwene ake atamulakwira?
-
Yosefe sanabwezere azichimwene ake koma anawakhululukira ataona kuti asintha.—Sal. 86:5; Luka 17:3, 4
-
Iye sanawasungire chakukhosi koma m’malomwake anatsanzira Yehova amene amakhululuka ndi mtima wonse.—Mika 7:18, 19
Kodi ndingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yokhululuka?