Ezekieli Anasangalala Kulengeza Uthenga wa Mulungu
M’masomphenya, Yehova anapatsa Ezekieli mpukutu n’kumuuza kuti adye. Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani?
-
Ezekieli ankafunika kuwerenga komanso kumvetsa bwino uthenga wa Mulungu. Kusinkhasinkha zimene ankawerenga mumpukutu kunachititsa kuti uthenga wake umufike pamtima ndipo izi zinamulimbikitsa kuti aziuza ena
-
Ezekieli ankamva kuti mpukutuwo unkatsekemera chifukwa choti anasangalala ndi ntchito imene anapatsidwa