CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Chilamulo Chinkasonyeza Bwanji Kuti Yehova Amaganizira Anthu Osauka?
Aisiraeli ankathandiza anzawo omwe anali osauka komanso omwe analibe cholowa (De 14:28, 29; it-2 1110 ¶3)
M’chaka cha Sabata, Aisiraeli omwe anali ndi ngongole ankakhala ‘omasuka’ ku ngongoleyo (De 15:1-3; it-2 833)
Mwisiraeli yemwe anadzigulitsa kukhala kapolo, ankagwira ntchito ya ukapolo kwa zaka 6 koma m’chaka cha 7 ankamasulidwa komanso ankapatsidwa mphatso ndi mbuye wake (De 15:12-14; it-2 978 ¶6)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimaganizira Akhristu omwe akufunika kuthandizidwa?’