February 3-9
MASALIMO 144-146
Nyimbo Na. 145 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Osangalala Ndi Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova”
(10 min.)
Yehova amadalitsa anthu amene amamudalira (Sl 144:11-15; w18.04 32 ¶3-4)
Timasangalala ndi chiyembekezo chathu (Sl 146:5; w22.10 28 ¶16-17)
Anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova adzakhala osangalala mpaka kalekale (Sl 146:10; w18.01 26 ¶19-20)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 145:15, 16—Kodi mavesiwa akutithandiza bwanji kuona mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi zinyama? (it-1 111 ¶9)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 144:1-15 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo wakuuzani kuti amaphunzira ku yunivesite. (lmd phunziro 1 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Gwiritsani ntchito vidiyo yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (lmd phunziro 7 mfundo 4)
6. Nkhani
(4 min.) lmd zakumapeto A mfundo 7—Mutu: Mkazi Ayenera ‘Kulemekeza Kwambiri Mwamuna Wake.’ (th phunziro 1)
Nyimbo Na. 59
7. Yehova Amafuna Kuti Tizisangalala
(10 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova ndi Mulungu wachimwemwe. (1Ti 1:11) Anatipatsa mphatso zambiri zabwino zomwe zimasonyeza kuti amatikonda komanso amafuna kuti tizisangalala. (Mla 3:12, 13) Taganizirani mphatso ziwiri izi, chakudya komanso kaphokoso kosangalatsa.
Onerani VIDIYO yakuti Chilengedwe Chimasonyeza Kuti Yehova Amafuna Tizisangalala—Chakudya Chokoma Komanso Kaphokoso Kosangalatsa. Kenako funsani funso ili:
-
Kodi mphatso ya chakudya komanso kaphokoso kosangalatsa zimatitsimikizira bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizisangalala?
Werengani Salimo 32:8. Kenako funsani funso ili:
-
Kodi kudziwa kuti Yehova amafuna kuti muzisangalala kumakuthandizani bwanji kuti muzimvera malangizo ake omwe amapereka kudzera m’Baibulo komanso gulu lake?
8. Zofunika Pampingo
(5 min.)
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 22 ¶1-6