January 29–February 4
YOBU 40-42
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Zimene Tikuphunzira Kuchokera pa Zimene Zinachitikira Yobu
(10 min.)
Muzikumbukira kuti mumadziwa zinthu zochepa kwambiri poyerekezera ndi Yehova (Yob 42:1-3; w10 10/15 3-4 ¶4-6)
Muzikhala ofunitsitsa kulandira malangizo ochokera kwa Yehova ndi gulu lake (Yob 42:5, 6; w17.06 25 ¶12)
Yehova amadalitsa anthu omwe amakhalabe okhulupirika ngakhale akukumana ndi mavuto (Yob 42:10-12; Yak 5:11; w22.06 25 ¶17-18)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Yob 42:7—Kodi zimene anzake atatu a Yobu ankalankhula, zikusonyeza kuti kwenikweni ankatsutsa ndani, nanga kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji kuti tizipirira pamene tikunyozedwa? (it-2 808)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yob 42:1-17 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Lalikirani kwa munthu amene si Mkhristu. (lmd phunziro 5 mfundo 3)
5. Kuphunzitsa Anthu
6. Nkhani
(4 min.) lmd zakumapeto A mfundo 2—Mutu: Dziko Lapansili Silidzawonongedwa. (th phunziro 13)
Nyimbo Na. 108
7. Muzithandiza Ena Kuona Kuti Yehova Amawakonda
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Timasangalala kwambiri kulambira Mulungu yemwe ndi chikondi. (1Yo 4:8, 16) Chikondi cha Yehova chimatithandiza kuti tikhale anzake komanso timuyandikire. Monga nkhosa za Yehova, tonse timamva kuti iye amatikonda.
Timachita zonse zimene tingathe kuti tizitsanzira chikondi cha Yehova pochita zinthu ndi anthu a m’banja lathu, Akhristu anzathu komanso anthu ena. (Yob 6:14; 1Yo 4:11) Tikamasonyeza ena chikondi, timawathandiza kuti adziwe Yehova n’kumuyandikira. Koma tikamalephera kuwasonyeza chikondi, zingawavute kukhulupirira kuti Yehova amawakonda.
Onerani VIDIYO yakuti Tinapeza Chikondi Chachikhristu M’banja la Yehova. Kenako funsani funso lotsatirali:
Kodi nkhani ya Lei Lei ndi Mimi yakuphunzitsani chiyani pa kufunika kosonyeza ena chikondi?
Kodi tingatani kuti tithandize Akhristu anzathu kuti azimva kuti Yehova amawakonda?
-
Tiziwaona kuti ndi nkhosa zamtengo wapatali za Yehova.—Sl 100:3
-
Tizilankhula nawo mowalimbikitsa.—Aef 4:29
-
Tizichita nawo zinthu mosonyeza kuti tikuwamvetsa bwino.—Mt 7:11, 12
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 5 ¶1-8, bokosi patsamba 39