MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Mwamuna ndi Mkazi Wake Angachite Kuti Alimbitse Chikondi M’banja Lawo
Abulahamu ndi Sara ndi chitsanzo chabwino kwa anthu okwatirana pa nkhani yokondana komanso kulemekezana. (Gen. 12:11-13; 1 Pet. 3:6) Komabe iwo sanali angwiro choncho ankafunika kupirira mayesero osiyanasiyana. Kodi anthu a pabanja angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara?
Muzilankhulana bwino. Muziyankha modzichepetsa mwamuna kapena mkazi wanu akalankhula mawu enaake chifukwa chokhumudwa. (Gen. 16:5, 6) Muzipeza nthawi yochitira zinthu limodzi. Mawu komanso zochita zanu zizisonyeza kuti mumamukonda mnzanuyo. Koposa zonse, muzilola kuti Yehova azitsogolera banja lanu pophunzira mawu ake, kupemphera komanso kuchitira limodzi zinthu zokhudza kulambira. (Mlal. 4:12) Mabanja olimba amalemekezetsa Yehova, yemwe anayambitsa banja.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE MUNGACHITE KUTI MULIMBITSE CHIKONDI M’BANJA LANU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
N’chiyani chikusonyeza kuti Shaan ndi Kiara sakukondananso ngati kale?
-
N’chifukwa chiyani kulankhulana momasuka kuli kofunika m’banja?
-
Kodi chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara chinathandiza bwanji Shaan ndi Kiara?
-
Kodi Shaan ndi Kiara anachita chiyani kuti banja lawo liyambenso kuyenda bwino?
-
N’chifukwa chiyani anthu okwatirana sayenera kuyembekezera kuti azichita zinthu mosalakwitsa chilichonse?
Banja lanu likhoza kumayenda bwino