NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU December 2017
Zitsanzo za Ulaliki
Zitsanzo za Ulaliki wa Galamukani! ndiponso kuphunzitsa choonadi chokhudza imfa. Gwiritsani ntchito zitsanzozi kuti mupange ulaliki wanuwanu.
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Funafunani Yehova Tsiku la Mkwiyo Wake Lisanafike
Kuti tidzapulumuke patsiku la mkwiyo wa Yehova, tiyenera kumvera malangizo amene Zefaniya anapereka.
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
‘Gwirani Chovala cha Munthu Amene ndi Myuda’
Anthu a mitundu yonse akubwera kudzalambira Yehova limodzi ndi Akhristu odzozedwa. Kodi tingathandize Akhristu odzozedwa m’njira ziti?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Munthu Aliyense wa M’gawo Lanu
Timafunitsitsa kulalikira uthenga wabwino kwa munthu aliyense wa m’gawo lathu. Kodi tingachite bwanji zimenezi?
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Musachoke ‘M’chigwa cha Pakati pa Mapiri’
Kodi ‘chigwa cha pakati pa mapiri’ chikuimira chiyani? Nanga kodi anthu amathawira bwanji kuchigwa cha chitetezochi?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mbali Yatsopano pa Misonkhano ya Mkati mwa Mlungu
Muzigwiritsa ntchito mbali ya mfundo zimene ndikuphunzira komanso zithunzi ndi mavidiyo, zomwe zikupezeka mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi la Study Edition la pa intaneti, kuti muzipindula kwambiri mukamakonzekera misonkhano komanso kuti muyandikire kwambiri Yehova.
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Ukwati Wanu Umakondweretsa Yehova?
M’nthawi ya Malaki, Yehova sankavomereza kulambira kwa munthu amene wachitira zachinyengo mwamuna kapena mkazi wake. Kodi anthu okwatirana angasonyeze bwanji kuti ndi okhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wawo?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Chikondi Chenicheni
Yehova amafuna kuti ukwati uzikhala mgwirizano wa moyo wonse. Iye amapereka mfundo zomwe zingathandize Akhristu kusankha munthu wabwino wokwatirana naye komanso kukhala ndi banja losangalala.