Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

August 24-30

EKISODO 19-20

August 24-30

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • Mmene Malamulo 10 Amakukhudzirani”: (10 min.)

    • Eks 20:3-7​—Muzilemekeza Yehova komanso muzimulambira mosagawanika (w89 11/15 6 ¶1)

    • Eks 20:8-11​—Muziona kuti zinthu zauzimu ndi zofunika kwambiri pa moyo wanu

    • Eks 20:12-17​—Muzilemekeza anthu (w89 11/15 6 ¶2-3)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)

    • Eks 19:5, 6​—N’chifukwa chiyani mtundu wakale wa Isiraeli unataya mwayi wokhala ‘ufumu wa ansembe’? (it-2 687 ¶1-2)

    • Eks 20:4, 5​—Kodi zikutanthauza chiyani kuti Yehova amalanga ana ndi zidzukulu “chifukwa cha zolakwa za abambo” awo? (w04 3/15 27 ¶1)

    • Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 19:1-19 (th phunziro 10)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 91

  • Kodi Ndingatani Kuti Makolo Anga Azindilolako Kuchita Zinthu Zina?: (6 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yamakatuniyi. Kenako funsani achinyamata mafunso otsatirawa: Kodi mungatani kuti makolo anu azikudalirani kwambiri? Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwalakwitsa zinazake? N’chifukwa chiyani kulemekeza makolo kumathandiza kuti azikulolani kuchita zinthu zambiri?

  • Muzilemekeza Makolo Anu Omwe ndi Okalamba: (9 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi ndi mavuto otani amene angabwere makolo akamakalamba? N’chifukwa chiyani achibale akuyenera kumasukirana akamakambirana za thandizo limene makolo awo akufunikira? Kodi ana angasonyeze bwanji kuti akulemekeza makolo awo pomwe akuwasamalira?

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 97

  • Mawu Omaliza (Osapitirira 3 min.)

  • Nyimbo Na. 80 ndi Pemphero