Zitsanzo za Ulaliki
GALAMUKANI!
Funso: Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi?
Lemba: Mlal. 4:6
Perekani Magaziniyo: Galamukani! iyi ili ndi mfundo zothandiza zokhudza mmene tingagwiritsire ntchito bwino nthawi.
KUPHUNZITSA CHOONADI
Funso: Kodi Mulungu anatilenga chifukwa chiyani?
Lemba: Sal. 37:29
Zoona Zake: Mulungu analenga anthu n’cholinga choti azikhala ndi moyo padzikoli mpaka kalekale.
UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU
Funso: Kodi mukuganiza kuti uthenga wabwino tingaupeze kuti? [Onetsani vidiyo yakuti Kodi Mungakonde Kumva Uthenga Wabwino?]
Lemba: Yes. 52:7
Perekani Kabuku: Kabuku aka kali ndi “uthenga wabwino wa zinthu zabwino” chifukwa muli mfundo za m’Baibulo.
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.