Udindo Waukulu wa Mlonda
Anthu amene ankagwira ntchito ya ulonda ankakhala pamwamba pa mpanda kapena pansanja ndipo ankachenjeza anthu ngati kukubwera zoopsa. Yehova mophiphiritsira anasankha Ezekieli kuti akhale “mlonda wa nyumba ya Isiraeli.”
-
Ezekieli anachenjeza Aisiraeli kuti adzawonongedwa ngati sasiya kuchita zoipa
Kodi masiku ano timalengeza uthenga wotani wochokera kwa Yehova?
-
Ngati akanapereka chenjezo, Ezekieli akanapulumutsa moyo wake komanso wa anthu ena
Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kuti tizilengeza mwachangu uthenga umene Yehova watipatsa?