Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Ndingadzachitenso Liti Upainiya Wothandiza?

Kodi Ndingadzachitenso Liti Upainiya Wothandiza?

Masomphenya a Ezekieli onena za kachisi amasonyeza kuti anthu a Yehova amafunika kuti azipereka nsembe zaufulu. Ndiye kodi tingatani kuti nafenso tizipereka nsembe zotamanda Mulungu?​—Aheb. 13:15, 16.

Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kulembetsa upainiya wothandiza. Chaka cha utumiki cha 2018 chidzakhala ndi miyezi yambiri yokhala ndi masiku a Loweruka kapena Lamlungu okwana 5. Zimenezi zidzathandiza kwambiri anthu amene amagwira ntchito yolembedwa ndipo amapeza mpata wolalikira tsiku Loweruka ndi Lamlungu lokha basi. Komanso ofalitsa akhoza kusankha kuchita upainiya wa maola 30 kapena 50 m’miyezi ya March ndi April ndiponso m’mwezi umene woyang’anira dera akuchezera mpingo wawo.

Nanga bwanji ngati sitingathe kuchita upainiya wothandiza chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu? Tikhoza kungoyesetsa kuwonjezera luso lathu komanso zimene timachita mu utumiki. Mulimonse mmene zinthu zilili pamoyo wathu, tiyeni tidzasonyeze kuti timakonda kwambiri Yehova pomupatsa zinthu zabwino zimene tingakwanitse m’chaka cha utumiki cha 2018.​—Hos. 14:2.

Kodi ndingatani kuti ndizilalikira mwakhama ngati Mlongo Sabina Hernández?

ONERANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA AMANDITHANDIZA KUCHITA ZINTHU ZAMBIRI, NDIPO KENAKO MUYANKHE MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi n’chiyani chimathandiza Mlongo Sabina kuti azichita zambiri potumikira Yehova?

  • Kodi chitsanzo cha Mlongo Sabina chingakulimbikitseni bwanji?

  • M’chaka cha utumiki cha 2018, ndi mwezi uti umene mukufuna kudzachita upainiya wothandiza?