April 6-12
Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu Udzachitika Lachiwiri pa 7 April, 2020
Chaka chilichonse panyengo ya Chikumbutso, Akhristu ambiri amaganizira chikondi chachikulu chimene Yehova ndi Mwana wake Yesu Khristu anatisonyeza. (Yoh 3:16; 15:13) Gwiritsani ntchito tchati chili m’munsichi kuti mupeze malemba omwe akufotokoza zimene zinachitika m’nthawi yomaliza ya utumiki wa Yesu ku Yerusalemu. Zomwe zinachitikazo zinafotokozedwa m’chigawo 6 cha buku la Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo. Kodi chikondi chomwe Mulungu komanso Khristu anakusonyezani chimakulimbikitsani bwanji?—2Ak 5:14, 15; 1Yo 4:16, 19.
MASIKU OMALIZA A UTUMIKI WA YESU KU YERUSALEMU
Nthawi |
Malo |
Zimene Zinachitika |
Mateyu |
Maliko |
Luka |
Yohane |
---|---|---|---|---|---|---|
33 C.E., Nisani 8 (1-2 April, 2020) |
Betaniya |
Yesu anafika ku Betaniya kutatsala masiku 6 kuti Pasika achitike |
|
|
|
|
Nisani 9 (2-3 April, 2020) |
Betaniya |
Mariya anathira Yesu mafuta m’mutu ndi m’mapazi |
|
|||
Betaniya-Betefage-Yerusalemu |
Analowa mu Yerusalemu mwaulemerero, atakwera bulu |
|||||
Nisani 10 (3-4 April, 2020) |
Betaniya-Yerusalemu |
Anatemberera mtengo wa mkuyu; kenako anayeretsanso kachisi |
|
|||
Yerusalemu |
Ansembe aakulu ndi alembi anakonza chiwembu choti aphe Yesu |
|
|
|||
Mawu a Yehova anamveka; Yesu ananeneratu za imfa yake; Ayuda sanamukhulupirire ndipo zimenezi zinakwaniritsa ulosi wa Yesaya |
|
|
|
|||
Nisani 11 (4-5 April, 2020) |
Betaniya-Yerusalemu |
Anaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito mtengo wa mkuyu womwe unafota |
|
|
||
Yerusalemu, kachisi |
Anthu anakaikira ulamuliro wa Khristu; fanizo la ana awiri aamuna |
|
||||
Mafanizo: alimi omwe anapha anthu, phwando la ukwati |
|
|||||
Yesu anayankha mafunso okhudza Mulungu komanso Kaisara, kuuka kwa akufa, lamulo lalikulu kwambiri |
|
|||||
Yesu anafunsa anthu ngati Khristu ali mwana wa Davide |
|
|||||
Anadzudzula mwamphamvu alembi ndi Afarisi |
|
|||||
Anaona mkazi wamasiye akupereka ndalama |
|
|
||||
Phiri la Maolivi |
Ananena za chizindikiro cha kukhalapo kwake |
|
||||
Mafanizo: anamwali 10, matalente, nkhosa ndi mbuzi |
|
|
|
|||
Nisani 12 (5-6 April, 2020) |
Yerusalemu |
Atsogoleri achiyuda anakonza zoti amuphe |
|
|||
Yudasi anakonza zomupereka |
|
|||||
Nisani 13 (6-7 April, 2020) |
Pafupi ndi Yerusalemu komanso mkati mwake |
Anakonzekera Pasika womaliza |
|
|||
Nisani 14 (7-8 April, 2020) |
Yerusalemu |
Anadya Pasika ndi atumwi ake |
|
|||
Anasambitsa mapazi a atumwi ake |
|
|
|
|||
Yesu ananena kuti Yudasi ndi yemwe adzamupereke ndipo anamuuza kuti achoke |
||||||
Anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (1Ak 11:23-25) |
|
|||||
Ananeneratu kuti Petulo adzamukana komanso kuti atumwi adzabalalika |
||||||
Analonjeza kuti adzatumiza mthandizi; fanizo la mpesa; anapereka lamulo la chikondi; anapemphera komaliza ndi atumwi ake |
|
|
|
|||
Getsemane |
Anavutika maganizo; anaperekedwa ndi kumangidwa |
|||||
Yerusalemu |
Anafunsidwa mafunso ndi Anasi; anazengedwa mlandu ndi Kayafa, Khoti Lalikulu la Ayuda; Petulo anamukana |
|||||
Yudasi amene anapereka Yesu anadzimangirira (Mac 1:18, 19) |
|
|
|
|||
Anaonekera kwa Pilato, Herode, kenako anabwereranso kwa Pilato |
||||||
Pilato anayesetsa kuti amumasule koma Ayuda anasankha kuti awamasulire Baraba; anaweruzidwa kuti aphedwe mochita kupachikidwa pamtengo |
||||||
(cha m’ma 3 koloko madzulo) |
Gologota |
Anafa atamupachika pamtengo |
||||
Yerusalemu |
Anatsitsa thupi lake pamtengo n’kukaliika m’manda |
|||||
Nisani 15 (8-9 April, 2020) |
Yerusalemu |
Ansembe ndi Afarisi anatseka pamandapo n’kuikapo alonda |
|
|
|
|
Nisani 16 (9-10 April, 2020) |
Yerusalemu ndi madera apafupi; Emau |
Yesu anaukitsidwa; anaonekera maulendo 5 kwa ophunzira ake |
||||
Pambuyo pa Nisani 16 |
Yerusalemu; Galileya |
Anaonekeranso maulendo angapo kwa ophunzira ake (1Ak 15:5-7; Mac 1:3-8); anawalangiza; ndi kuwalamula kuti agwire ntchito yophunzitsa anthu |
|
|