NDANDANDA YA UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU April 2018
Zimene Tinganene
Zimene tinganene zokhudza Baibulo komanso zimene tingachite kuti tizikhala osangalala.
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kufanana Komanso Kusiyana Komwe Kulipo Pakati pa Mwambo wa Pasika ndi Chikumbutso
Ngakhale kuti zomwe zinkachitika pa mwambo wa Pasika sizinkaimira zimene zimachitika pa Chikumbutso, zimene zinkachitika pamwambowu zingatithandize kumvetsa mfundo zina.
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Tingamvere Bwanji Lamulo Lakuti, Pitani Mukaphunzitse Anthu?
Kuphunzitsa anthu kumatanthauza kuwathandiza kuti azisunga zinthu zonse zimene Yesu analamula. Lamulo loti tiziphunzitsa anthu limaphatikizapo kuthandiza wophunzira wathu kuti azigwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa komanso kutsatira chitsanzo chake.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kulalikira Komanso Kuphunzitsa N’kofunika Kwambiri Kuti Tipange Ophunzira
Yesu analamula otsatira ake kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Kodi tingathandize bwanji anthu kuti apite patsogolo mwauzimu?
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Machimo Ako Akhululukidwa”
Kodi tikuphunzira chiyani pa chozizwitsa chopezeka pa Maliko 2:5-12? Kodi nkhani imeneyi ingatithandize bwanji kupirira tikamadwala?
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata
N’chifukwa chiyani Yesu anakwiya kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda? Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kudziwa ngati tikutsanzira Yesu pa nkhani yosonyeza chifundo?
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Yesu Ali ndi Mphamvu Zoukitsa Anthu Amene Anamwalira
Tikamaganizira nkhani za m’Baibulo za anthu amene anaukitsidwa, sitingakayikire zoti anthu amene timawakonda adzaukitsidwa m’tsogolo.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tizigwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa
Kuti tiziphunzitsa anthu mwaluso, timafunika kuphunzira mmene tingagwiritsire ntchito zida zathu zophunzitsira. Kodi chida chathu chachikulu chophunzitsira ndi chiyani? Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa?