A7-H
Zinthu Zikuluzikulu Zimene Yesu Anachita Ali Padziko Lapansi—Utumiki Womaliza wa Yesu mu Yerusalemu (Gawo 2)
NTHAWI |
MALO |
ZIMENE ZINACHITIKA |
MATEYU |
MALIKO |
LUKA |
YOHANE |
---|---|---|---|---|---|---|
Nisani 14 |
Yerusalemu |
Yesu anaulula kuti Yudasi adzamupereka ndipo anamuuza kuti achoke |
||||
Anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo (1Akor. 11:23-25) |
||||||
Ananeneratu kuti Petulo adzamukana komanso kuti atumwi adzabalalika |
||||||
Anati adzatumiza mthandizi; fanizo la mpesa; lamulo loti tizikondana; anapemphera komaliza ndi atumwi ake |
||||||
Getsemane |
Yesu anavutika maganizo; anaperekedwa ndi kumangidwa |
|||||
Yerusalemu |
Anasi anamufunsa; Kayafa ndi Khoti Lalikulu la Ayuda anamuzenga mlandu; Petulo anamukana |
|||||
Yudasi amene anamupereka uja anadzimangirira (Mac. 1:18, 19) |
||||||
Anaonekera kwa Pilato, kenako kwa Herode nʼkubwereranso kwa Pilato |
||||||
Pilato anayesetsa kuti amumasule koma Ayuda anasankha Baraba; anaweruzidwa kuti aphedwe pomukhomerera pamtengo |
||||||
(c. 3:00 madzulo, Lachisanu) |
Gologota |
Anafera pamtengo wozunzikirapo |
||||
Yerusalemu |
Anachotsa mtembo wa Yesu pamtengo nʼkukauika mʼmanda |
|||||
Nisani 15 |
Yerusalemu |
Ansembe ndi Afarisi anaika alonda pamanda nʼkutsekapo |
||||
Nisani 16 |
Yerusalemu ndi madera apafupi; Emau |
Yesu anaukitsidwa; anaonekera kwa ophunzira ake ka 5 |
||||
Pambuyo pa Nisani 16 |
Yerusalemu; Galileya |
Anaonekeranso kwa ophunzira ake kangapo (1Akor. 15:5-7; Mac. 1:3-8); anaphunzitsa; analamula ophunzira ake kuti aphunzitse anthu kukhala ophunzira ake |
||||
Iyari 25 |
Phiri la Maolivi, pafupi ndi Betaniya |
Yesu anakwera kumwamba, tsiku la 40 ataukitsidwa (Mac. 1:9-12) |