Yobu 21:1-34

  • Yankho la Yobu (1-34)

    • ‘Nʼchifukwa chiyani anthu oipa zinthu zimawayendera bwino?’ (7-13)

    • Anaonetsa kuti anzakewo anali achinyengo (27-34)

21  Yobu anayankha kuti:  2  “Mvetserani mwatcheru zimene ndikufuna kunena.Mukachita zimenezi ndiye kuti munditonthoza.  3  Ndilezereni mtima pamene ndikulankhula.Ndikamaliza kulankhula, mukhoza kuyamba kundinyoza.+  4  Kodi madandaulo anga akupita kwa munthu? Zikanakhala choncho, kodi ndikanakhalabe woleza mtima?*  5  Tandiyangʼaneni ndipo mudabwa,Gwirani pakamwa panu.  6  Ndikaziganizira, zikumandisokoneza,Ndipo thupi langa lonse likumanjenjemera.  7  Nʼchifukwa chiyani oipa amakhalabe ndi moyo,+Amakalamba komanso amalemera* kwambiri?+  8  Ana awo amakhala nawo limodzi nthawi zonse,Ndipo amakhala ndi moyo wautali moti amaona zidzukulu zawo.  9  Nyumba zawo nʼzotetezeka ndipo saopa chilichonse,+Mulungu sawalanga ndi ndodo yake. 10  Ngʼombe zawo zamphongo sizilephera kupereka bere.Ngʼombe zawo zazikazi zimabereka ndipo sizibereka ana akufa. 11  Anyamata awo amathamangira panja ngati nkhosa,Ndipo ana awo amadumphadumpha. 12  Iwo amaimba pogwiritsa ntchito maseche ndi azeze.Ndipo amasangalala akamva kulira kwa chitoliro.+ 13  Masiku awo onse amakhala moyo wabwino,Ndipo amapita ku Manda* mwamtendere.* 14  Koma iwo amauza Mulungu woona kuti, ‘Tisiyeni! Sitikufuna kudziwa njira zanu.+ 15  Kodi Wamphamvuyonse ndi ndani kuti timutumikire?+ Ndipo kodi tingapindule chiyani ngati titamudziwa?’+ 16  Koma ndikudziwa kuti alibe mphamvu zochititsa kuti zinthu ziwayendere bwino pa moyo wawo.+ Zimene anthu oipa amaganiza nʼzosiyana* ndi zimene ndimaganiza.+ 17  Kodi nyale ya oipa imazimitsidwa kangati?+ Ndipo tsoka limawagwera kangati? Kodi Mulungu amawawononga kangati atakwiya? 18  Kodi iwo anayamba akhalapo ngati udzu wouluzika ndi mphepoKapena ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo yamkuntho? 19  Mulungu adzalanga ana a munthu woipa chifukwa cha zolakwa za bambo awo. Koma Mulungu amulangenso iyeyo kuti adziwe kulakwa kwake.+ 20  Maso ake aone iye akamawonongedwa,Ndipo adzamwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse.+ 21  Ngati chiwerengero cha masiku a moyo wake chitachepa,*Sadzasamala zimene zidzachitikire anthu amʼnyumba yake iyeyo atapita.+ 22  Kodi pali aliyense amene angaphunzitse Mulungu chilichonse,*+Pamene Mulunguyo ndi amene amaweruza ngakhale anthu apamwamba?+ 23  Munthu wina amafa adakali ndi mphamvu+Ali pa mtendere komanso wopanda nkhawa,+ 24  Ntchafu zake zitafufuma ndi mafuta,Ndipo mafupa ake ali olimba.* 25  Koma munthu winanso amafa ali ndi nkhawa zazikulu,*Asanalawepo zinthu zabwino. 26  Iwo adzagona limodzi mʼfumbi,+Ndipo onsewo adzakhala mphutsi zokhazokha.+ 27  Inetu ndikudziwa bwino zimene mukuganiza,Ndiponso mapulani amene mukupanga kuti mundichitire zoipa.+ 28  Chifukwa mukunena kuti, ‘Kodi nyumba ya munthu wolemekezeka ili kuti,Nanga tenti imene munthu woipa ankakhala ili kuti?’+ 29  Kodi simunafunse anthu apaulendo? Kodi simunafufuze mosamala zimene amanena,* 30  Zoti munthu woipa amapulumuka pa tsiku la tsoka,Ndiponso kuti pa tsiku la mkwiyo amapulumutsidwa? 31  Ndi ndani angamuuze pamasomʼpamaso kuti akuyenda njira yoipa,Ndipo ndi ndani angamubwezere pa zimene wachita? 32  Akadzapita naye kumanda,Anthu adzachezera pamanda ake. 33  Dothi lamʼchigwa* limene adzamukwirire nalo lidzakhala lotsekemera kwa iye,+Ndipo anthu onse adzamutsatira*+Mofanana ndi anthu osawerengeka amene anapita iye asanapite. 34  Ndiye nʼchifukwa chiyani mukunditonthoza ndi mawu osathandiza?+ Ndipo mayankho anu ndi mabodza okhaokha.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kodi mzimu wanga ukanakhalabe woleza mtima?”
Kapena kuti, “amakhala amphamvu.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼkanthawi kochepa,” kutanthauza kuti amafa mwamsanga ndipo samva kupweteka.
Kapena kuti, “Malangizo a anthu oipa ndi osiyana; Mapulani a anthu oipa ndi osiyana.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngati miyezi yake itadulidwa pakati.”
Kapena kuti, “amene angaphunzitse Mulungu nzeru.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo mafuta a mʼmafupa ake ali ofewa.”
Kapena kuti, “amafa mtima ukumupweteka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zizindikiro zawo.”
Kapena kuti, “lamʼkhwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo adzakoka anthu onse kuti amutsatire.”