Yesaya 59:1-21
59 Dzanja la Yehova silinafupike moti nʼkulephera kupulumutsa,+Komanso khutu lake silinagonthe* moti nʼkulephera kumva.+
2 Ayi si choncho. Koma zolakwa zanu nʼzimene zakulekanitsani ndi Mulungu wanu.+
Machimo anu ndi amene amuchititsa kuti akubisireni nkhope yake,Ndipo sakufuna kumva zimene mukunena.+
3 Chifukwa mʼmanja mwanu mwaipitsidwa ndi magazi+Ndipo zala zanu zaipitsidwa ndi zolakwa.
Milomo yanu imalankhula zabodza+ ndipo lilime lanu limanena zinthu zopanda chilungamo.
4 Palibe amene amafuula poikira kumbuyo chilungamo,+Ndipo palibe amene amalankhula zoona akapita kukhoti.
Iwo amakhulupirira zinthu zachabechabe+ ndipo amalankhula zopanda pake.
Iwo atenga pakati pa mavuto ndipo abereka zopweteka.+
5 Iwo aikira mazira a njoka yapoizoni,Ndipo amaluka ukonde wa kangaude.+
Aliyense amene angadye mazira awowo adzafa,Ndipo mʼdzira limene lasweka mumatuluka mphiri.
6 Ukonde wawo wa kangaude sudzakhala chovala chawo,Ndipo zochita zawo sizingawathandize.+
Ntchito zawo nʼzopweteka ena,Ndipo mʼmanja mwawo muli ntchito zachiwawa.+
7 Mapazi awo amathamangira kukachita zoipa,Ndipo amafulumira kukhetsa magazi a anthu osalakwa.+
Maganizo awo ndi maganizo oipa.Zonse zimene amachita zimakhala zowononga ndiponso zobweretsa mavuto.+
8 Njira ya mtendere sakuidziwa,Ndipo mʼnjira zawo mulibe chilungamo.+
Misewu yawo aikhotetsakhotetsa.Palibe munthu aliyense woyenda mmenemo amene adzadziwe mtendere.+
9 Nʼchifukwa chake chilungamo chatitalikira kwambiri,Ndipo zinthu zolungama sizikutipeza.
Tikuyembekezera kuwala, koma mʼmalomwake tikungoona mdima.Tikuyembekezera tsiku lowala, koma tikupitirizabe kuyenda mumdima waukulu.+
10 Tikungopapasa khoma ngati anthu amene ali ndi vuto losaona,Tikungopapasapapasa ngati anthu opanda maso.+
Tikupunthwa masanasana ngati kuti tili mumdima wamadzulo.Pakati pa anthu amphamvu tikungokhala ngati anthu akufa.
11 Tonsefe tikungolira ngati zimbalangondoNdipo tikungokhalira kubuula momvetsa chisoni ngati njiwa.
Tikuyembekezera chilungamo koma sichikupezeka.Tikuyembekezera chipulumutso koma chili kutali ndi ife.
12 Chifukwa zolakwa zathu zachuluka pamaso panu,+Tchimo lathu lililonse likupereka umboni wotsutsana nafe.+
Zolakwa zathu zili pa ife,Ndipo zochimwa zathu tikuzidziwa bwino.+
13 Ife tachimwa ndipo tamukana Yehova.Tabwerera mʼmbuyo nʼkumusiya Mulungu wathu.
Tanena zinthu zopondereza ena komanso zopanduka.+Taganizira mabodza oti tinene ndipo talankhula mawu achinyengo mumtima mwathu.+
14 Chilungamo chabwezedwa mʼmbuyo,+Ndipo chilungamocho chaima patali.+Chifukwa choonadi chapunthwa* mʼbwalo lamumzinda,Ndipo zinthu zolungama zikulephera kulowamo.
15 Choonadi chasowa*+Ndipo aliyense wokana kuchita zoipa akulandidwa zinthu zake.
Yehova anaona zimenezi ndipo sanasangalale nazo,*Chifukwa panalibe chilungamo.+
16 Iye ataona kuti panalibe munthu aliyense woti nʼkuthandizapo,Anadabwa kwambiri kuti palibe amene akulowererapo.Choncho anapulumutsa anthu* ndi dzanja lake,Ndipo chilungamo chake nʼchimene chinamulimbikitsa kuchita zimenezo.
17 Choncho iye anavala chilungamo ngati chovala chamamba achitsulo,Ndiponso anavala chipewa cha chipulumutso* kumutu kwake.+
Anavala chilungamo ngati chovala kuti apereke chilango kwa adani ake+Ndipo kuchita zinthu modzipereka kwambiri kunali ngati chovala chake chodula manja.
18 Iye adzawapatsa mphoto chifukwa cha zimene achita:+
Adani ake adzawapatsa mkwiyo ndipo anthu otsutsana naye adzawapatsa chilango.+
Ndipo zilumba adzazipatsa chilango chogwirizana ndi zochita zawo.
19 Amene ali kolowera dzuwa adzaopa dzina la Yehova,Ndipo amene ali kotulukira dzuwa adzaopa ulemerero wake,Chifukwa iye adzabwera ngati mtsinje wothamanga,Umene ukuyendetsedwa ndi mzimu wa Yehova.
20 “Wowombola+ adzabwera+ ku Ziyoni,Adzabwera kwa mbadwa za Yakobo zimene zasiya zolakwa zawo,”+ akutero Yehova.
21 Yehova wanena kuti: “Koma pangano langa ndi iwowo ndi ili,+ mzimu wanga umene uli pa iwe ndi mawu anga amene ndaika mʼkamwa mwako, sizidzachotsedwa mʼkamwa mwako, mʼkamwa mwa ana ako* kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zako,* kuyambira panopa mpaka kalekale,” akutero Yehova.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “si lolemera.”
^ Kapena kuti, “kuona mtima kwapunthwa.”
^ Kapena kuti, “Kuona mtima kwasowa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo zinamuipira mʼmaso mwake.”
^ Kapena kuti, “anawachititsa kuti apambane.”
^ Kapena kuti, “cha kupambana.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu ya mbewu yako.”