Yesaya 41:1-29
41 “Zilumba inu, khalani chete* ndi kundimvetsera.Inu mitundu ya anthu, pezaninso mphamvu.
Bwerani pafupi ndi ine, kenako mulankhule.+
Tiyeni tikumane ndipo ndikuweruzani.
2 Kodi ndi ndani amene wapatsa mphamvu winawake kuchokera kotulukira dzuwa,*+Amene wamuitana mwachilungamo kuti ayandikire kumapazi ake,*Kuti amupatse mitundu ya anthuNdiponso kuti amuchititse kuti agonjetse mafumu?+
Kodi ndi ndani amene amawasandutsa fumbi pogwiritsa ntchito lupanga lake,Ndipo ndi ndani amene amawabalalitsa ngati mapesi ouluzika ndi mphepo pogwiritsa ntchito uta wake?
3 Iye amawathamangitsa, amadutsa popanda chilichonse chomusokonezaMʼnjira zimene mapazi ake sanayambe adutsamo.
4 Ndi ndani wachita zimenezi,Ndi ndani waitana mibadwo kuchokera pachiyambi?
Ndi ineyo Yehova, ndine Woyamba,+Ndipo kwa omalizira ndimakhala chimodzimodzi.”+
5 Zilumba zaona zimenezi ndipo zachita mantha.
Malekezero a dziko lapansi anayamba kunjenjemera.
Mitundu ya anthu inayandikira nʼkubwera.
6 Aliyense akuthandiza mnzakeNdipo akuuza mʼbale wake kuti: “Limba mtima.”
7 Choncho mmisiri wa mitengo akulimbikitsa mmisiri wa zitsulo.+Amene amawongola zitsulo ndi hamalaAkulimbikitsa munthu amene akusula zitsulo ndi hamala.
Ponena za ntchito yowotcherera zitsulo ndi mtovu, iye akuti: “Zili bwino.”
Kenako amakhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
8 “Koma iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga,+Iwe Yakobo, amene ndakusankha,+Mbadwa* ya mnzanga Abulahamu.+
9 Iwe amene ndinakutenga kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+Ndiponso iwe amene ndinakuitana kuchokera kumadera akutali a dziko lapansi.
Ndinakuuza kuti, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga.+Ndakusankha ndipo sindinakutaye.+
10 Usachite mantha, chifukwa ndili ndi iwe.+
Usade nkhawa chifukwa ine ndine Mulungu wako.+
Ndikulimbitsa, ndithu ndikuthandiza,+Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.’
11 Taona! Onse amene amakupsera mtima adzachita manyazi ndipo adzanyozeka.+
Anthu amene akumenyana nawe adzawonongedwa ndipo adzatha.+
12 Anthu amene akulimbana nawe udzawafunafuna koma sudzawapeza.Anthu amene akumenyana nawe adzakhala ngati chinthu chimene kulibeko ndipo sadzakhalanso ngati kanthu.+
13 Chifukwa ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja,Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’+
14 “Usachite mantha, nyongolotsi* iwe Yakobo,+Inu amuna a mu Isiraeli, ineyo ndikuthandizani,” akutero Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli.
15 “Taona! Ndakusandutsa chopunthira mbewu,+Chida chatsopano chopunthira mbewu chokhala ndi mano akuthwa konsekonse.
Udzapondaponda mapiri nʼkuwaphwanyaNdipo zitunda udzazisandutsa mankhusu.
16 Udzapeta mapiri ndi zitundazoNdipo mphepo idzaziuluza.Mphepo yamkuntho idzazimwaza.
Iweyo udzasangalala chifukwa cha Yehova,+Ndipo udzadzitama chifukwa cha Woyera wa Isiraeli.”+
17 “Anthu ovutika ndi osauka akufunafuna madzi, koma sakuwapeza.
Lilime lawo lauma chifukwa cha ludzu.+
Ineyo Yehova ndidzawayankha.+
Ineyo Mulungu wa Isiraeli, sindidzawasiya.+
18 Ndidzachititsa kuti mitsinje yamadzi iyende mʼmapiri opanda zomera zilizonse+Komanso kuti akasupe atuluke mʼzigwa.+
Chipululu ndidzachisandutsa dambo lamadziNdipo dziko lopanda madzi ndidzalisandutsa akasupe amadzi.+
19 Mʼchipululu ndidzadzalamo mtengo wa mkungudza,Mtengo wa mthethe, mtengo wa mchisu ndi mtengo wa paini.+
Mʼchigwa chamʼchipululu ndidzadzalamo mtengo wa junipa,*Limodzi ndi mtengo wa ashi* komanso mtengo wofanana ndi mkungudza,+
20 Ndidzachita zimenezi kuti anthu onse aone ndipo adziwe,Amve ndiponso azindikireKuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi,Ndiponso kuti Woyera wa Isiraeli ndi amene wachititsa zimenezi.”+
21 “Bweretsani kuno mlandu wanu,” akutero Yehova.
“Fotokozani mfundo zanu,” ikutero Mfumu ya Yakobo.
22 “Tipatseni umboni ndipo mutiuze zinthu zimene zidzachitike.
Tiuzeni zokhudza zinthu zakale,*Kuti tiziganizire mozama nʼkudziwa tsogolo lake.
Kapena mutiuze zinthu zimene zikubwera.+
23 Tiuzeni zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo,Kuti tidziwe kuti ndinu milungu.+
Inde, chitani chinachake, chabwino kapena choipa,Kuti tidabwe tikachiona.+
24 Taonani! Inuyo ndi chinthu chopanda ntchito,Ndipo palibe chimene mwakwanitsa kuchita.+
Aliyense amene amasankha kukulambirani ndi wonyansa.+
25 Ine ndapatsa mphamvu winawake kuchokera kumpoto, ndipo abwera.+Iye adzachokera kotulukira dzuwa*+ ndipo adzaitana pa dzina langa.
Adzapondaponda olamulira* ngati akuponda dongo+Ngati woumba amene amapondaponda dongo laliwisi.
26 Kodi ndi ndani ananenapo zokhudza zimenezi kuchokera pachiyambi kuti tidziwe,Kapena kuchokera kalekale kuti tinene kuti, ‘Akunena zoonaʼ?+
Ndithu palibe amene analengeza zimenezi.
Palibe amene ananena chilichonse.
Palibe amene anamva chilichonse kuchokera kwa inu.”+
27 Ine ndinali woyamba kuuza Ziyoni kuti: “Tamverani zimene zidzachitike!”+
Ndipo ku Yerusalemu ndidzatumizako munthu wobweretsa uthenga wabwino.+
28 Koma ndinapitiriza kuyangʼana, ndipo panalibe aliyense.Pakati pa mafanowo panalibe aliyense amene akanapereka malangizo.
Ndipo ndinapitiriza kuwafunsa, koma palibe anayankha.
29 Onsewo ndi opanda ntchito.*
Ntchito zawo ndi zopanda pake.
Mafano awo opangidwa ndi zitsulo* ali ngati mphepo ndipo ndi opanda ntchito.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “khalani chete pamaso panga.”
^ Kapena kuti, “kuchokera kumʼmawa.”
^ Kutanthauza kumutumikira.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu.”
^ Kutanthauza wopanda chitetezo chilichonse komanso wonyozeka.
^ Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
^ Umenewu ndi mtengo waukulu umene umatalika mpaka mamita 15. Umakhala ndi masamba osabiriwira kwambiri ndi nthambi zotuwa ngati phulusa.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zoyambirira.”
^ Kapena kuti, “kuchokera kumʼmawa.”
^ Kapena kuti, “achiwiri kwa olamulira.”
^ Kapena kuti, “ndi chinthu chimene kulibe.”
^ Kapena kuti, “zitsulo zosungunula.”