Yesaya 11:1-16
11 Nthambi+ idzaphuka pachitsa cha Jese,+Ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzabereka zipatso.
2 Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye,+Mzimu wanzeru+ ndi womvetsa zinthu,Mzimu wopereka malangizo abwino ndi wamphamvu,+Mzimu wodziwa zinthu ndi woopa Yehova.
3 Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova.+
Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake,Kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake.+
4 Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka,Ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa apadziko lapansi.
Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake+Ndipo adzapha anthu oipa pogwiritsa ntchito mpweya* wamʼkamwa mwake.+
5 Chilungamo ndi kukhulupirikaZidzakhala lamba wamʼchiuno mwake.+
6 Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa kwa kanthawi,+Ndipo kambuku adzagona pansi ndi mbuzi yaingʼono,Mwana wa ngʼombe, mkango wamphamvu ndi nyama yonenepa zidzakhala pamodzi,*+Ndipo kamnyamata kakangʼono kadzazitsogolera.
7 Ngʼombe ndi chimbalangondo zidzadyera pamodziNdipo ana awo adzagona pansi pamodzi.
Mkango udzadya udzu ngati ngʼombe yamphongo.+
8 Mwana woyamwa adzasewera pa una wa mamba,Ndipo mwana amene anasiya kuyamwa adzapisa dzanja lake kudzenje la njoka yapoizoni.
9 Sizidzavulazana+Kapena kuwonongana mʼphiri langa lonse loyera,+Chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa YehovaNgati mmene madzi amadzazira mʼnyanja.+
10 Pa tsiku limenelo muzu wa Jese+ udzaimirira ngati chizindikiro kwa anthu.+
Anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awapatse malangizo,*+Ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.
11 Pa tsiku limenelo Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,* ku Hamati ndi mʼzilumba zamʼnyanja.+
12 Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu nʼkusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumakona 4 a dziko lapansi.+
13 Nsanje ya Efuraimu idzatha,+Ndipo anthu amene amadana ndi Yuda adzaphedwa.
Efuraimu sadzachitira nsanje Yuda,Ndiponso Yuda sadzadana ndi Efuraimu.+
14 Iwo adzatsika zitunda za* Afilisiti kumadzulo.Onsewa pamodzi, adzalanda katundu wa anthu a Kumʼmawa.
Adzatambasula dzanja lawo nʼkugonjetsa* Edomu+ ndi Mowabu,+Ndipo Aamoni adzawagonjera.+
15 Yehova adzagawa pakati* chigawo cha* nyanja ya Iguputo,+Ndipo adzayendetsa dzanja lake moopseza Mtsinje.*+
Pogwiritsa ntchito mpweya* wake wotentha, adzamenya timitsinje 7 tamtsinjewo,*Ndipo adzachititsa anthu kuwoloka atavala nsapato zawo.
16 Padzakhala msewu waukulu+ wochokera kudziko la Asuri woti mudzadutse anthu ake amene adzatsale,+Ngati mmene zinalili kwa Aisiraeli pamene ankatuluka mʼdziko la Iguputo.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mzimu.”
^ Mabaibulo ena amati, “zidzadyera limodzi.”
^ Kapena kuti, “Anthu a mitundu ina adzamufunafuna.”
^ Ameneyu ndi Babeloniya.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmapewa a.”
^ Kapena kuti, “adzasonyeza mphamvu zawo pa.”
^ Mabaibulo ena amati, “adzaphwetsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “lilime la.”
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
^ Kapena kuti, “mzimu.”
^ Mabaibulo ena amati, “adzaugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri.”