Oweruza 2:1-23

  • Chenjezo la mngelo wa Yehova (1-5)

  • Imfa ya Yoswa (6-10)

  • Oweruza anayamba kupulumutsa Isiraeli (11-23)

2  Kenako mngelo wa Yehova+ ananyamuka ku Giligala+ kupita ku Bokimu, ndipo anati: “Ndinakutulutsani mu Iguputo nʼkukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbirira makolo anu.+ Ndinanenanso kuti, ‘Sindidzaphwanya pangano langa ndi inu.+ 2  Inuyo musachite pangano ndi anthu okhala mʼdzikoli,+ ndipo mugwetse maguwa awo ansembe.’+ Koma inu simunamvere mawu anga.+ Nʼchifukwa chiyani mwachita zimenezi? 3  Nʼchifukwa chake ndinanena kuti, ‘Sindidzawathamangitsa pamaso panu,+ koma adzakhala msampha wanu,+ ndipo milungu yawo idzakhala ngati nyambo.’”+ 4  Mngelo wa Yehova atauza Aisiraeli mawu amenewa, anthuwo anayamba kulira mokweza. 5  Choncho malowo anawapatsa dzina lakuti Bokimu,* ndipo anaperekapo nsembe kwa Yehova. 6  Yoswa atauza Aisiraeliwo kuti azipita, aliyense anapita komwe kunali cholowa chake, kukatenga dzikolo kukhala lawo.+ 7  Anthuwo anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse amene Yoswa anali ndi moyo komanso masiku onse a akulu amene anakhalabe ndi moyo Yoswa atamwalira, omwe anaona zinthu zazikulu zimene Yehova anachitira Aisiraeli.+ 8  Kenako Yoswa, mtumiki wa Yehova, mwana wa Nuni, anamwalira ali ndi zaka 110.+ 9  Ndipo anamuika mʼmanda ku Timinati-heresi,+ mʼdera limene analandira monga cholowa chake, mʼdera lamapiri la Efuraimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.+ 10  Anthu onse a mʼbadwo umenewo anamwalira, ndipo panabwera mʼbadwo wina umene sunkadziwa Yehova kapena zimene iye anachitira Isiraeli. 11  Choncho Aisiraeli anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova ndipo anayamba kutumikira* Abaala.+ 12  Iwo anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa mʼdziko la Iguputo+ nʼkuyamba kutsatira milungu ya anthu owazungulira.+ Anayamba kugwadira milunguyo ndipo anakhumudwitsa Yehova.+ 13  Anasiya Yehova nʼkuyamba kutumikira Baala ndi zifaniziro za Asitoreti.+ 14  Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli, moti anawapereka mʼmanja mwa adani amene anawaukira nʼkutenga zinthu zawo.+ Iye anawagulitsa kwa adani awo owazungulira+ moti sanathe kulimbana nawo.+ 15  Kulikonse kumene ankapita, dzanja la Yehova linkawaukira ndi kuwabweretsera tsoka,+ mogwirizana ndi zimene Yehova ananena ndiponso zimene Yehova anawalumbirira,+ moti iwo ankavutika kwambiri.+ 16  Zikatero, Yehova ankawapatsa oweruza omwe ankawapulumutsa mʼmanja mwa adani.+ 17  Koma Aisiraeli sankamvera oweruzawo. Iwo ankachita chiwerewere ndi milungu ina ndi kuigwadira. Anasiya mwamsanga njira imene makolo awo anayendamo. Makolo awo ankamvera malamulo a Yehova,+ koma iwo sanachite zimenezo. 18  Yehova akawapatsa woweruza,+ Yehova ankakhala ndi woweruzayo, ndipo ankawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo pa nthawi yonse ya woweruzayo. Yehova ankawamvera chisoni+ akamva kulira kwawo chifukwa cha anthu omwe ankawapondereza+ komanso kuwachitira nkhanza. 19  Koma woweruza akamwalira, iwo ankayambiranso kuchita zoipa kuposa makolo awo. Ankatsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Iwo sanasiye zochita zawozo ndiponso unkhutukumve wawo. 20  Pamapeto pake, Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli+ ndipo anati: “Popeza mtundu umenewu waphwanya pangano langa+ limene ndinalamula makolo awo kuti alisunge, ndipo sanandimvere,+ 21  ine sindithamangitsanso pamaso pawo mtundu uliwonse pa mitundu imene Yoswa anaisiya pamene ankamwalira.+ 22  Ndichita zimenezi kuti ndiyese Aisiraeli ngati angasunge njira ya Yehova+ poyenda mʼnjirayo ngati mmene makolo awo anachitira.” 23  Choncho, Yehova analola mitundu imeneyi kukhalabe. Sanaithamangitse mwamsanga komanso sanaipereke mʼmanja mwa Yoswa.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza “Olira.”
Kapena kuti, “kulambira.”