Nehemiya 8:1-18
8 Anthu onse anasonkhana mogwirizana mʼbwalo lalikulu kutsogolo kwa Geti la Kumadzi.+ Anthuwo anauza Ezara+ wokopera Malemba* kuti abweretse buku la Chilamulo cha Mose+ chimene Yehova analamula Aisiraeli kuti azitsatira.+
2 Choncho Ezara wansembe anapititsa buku la Chilamulo kugulu la anthuwo.+ Panali amuna, akazi komanso aliyense amene akanatha kumvetsa zimene zikunenedwa. Limeneli linali tsiku loyamba la mwezi wa 7.+
3 Ezara anawerenga mokweza bukulo+ mʼbwalo lalikulu limene linali kutsogolo kwa Geti la Kumadzi, kuyambira mʼmawa mpaka masana. Anawerenga bukuli pamaso pa amuna, akazi ndiponso aliyense amene akanatha kumvetsa zimene zikunenedwa. Ndipo anthu ankamvetsera mwatcheru+ zimene zinali mʼbuku la Chilamuloli.
4 Ezara wokopera Malembayo,* anaima pansanja yamatabwa imene anaimanga chifukwa cha mwambowu. Kumanja kwake kunaima Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya. Kumanzere kwake kunali Pedaya, Misayeli, Malikiya,+ Hasumu, Hasi-badana, Zekariya ndi Mesulamu.
5 Ezara anatsegula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza anaima pamalo okwera kusiyana ndi anthu onse. Pamene ankatsegula bukulo, anthu onse anaimirira.
6 Kenako Ezara anatamanda Yehova Mulungu woona, Mulungu wamkulu. Atatero anthu onse ananena kuti, “Ame! Ame!”*+ ndipo anakweza manja awo mʼmwamba. Ndiyeno anthuwo anagwada nʼkuwerama pamaso pa Yehova mpaka nkhope zawo kufika pansi.
7 Yesuwa, Bani, Serebiya,+ Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseya, Kelita, Azariya, Yozabadi,+ Hanani ndi Pelaya, omwe anali Alevi, ankafotokozera anthu Chilamulocho,+ anthuwo ataimirira.
8 Iwo anapitiriza kuwerenga bukulo mokweza. Anapitiriza kuwerenga Chilamulo cha Mulungu woona, kuchifotokoza momveka bwino ndi kumveketsa tanthauzo lake. Choncho anathandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene ankawerenga.+
9 Ndiyeno Nehemiya, yemwe pa nthawiyo anali bwanamkubwa,* Ezara+ wansembe ndi wokopera Malemba,* komanso Alevi amene ankapereka malangizo kwa anthu, anauza anthuwo kuti: “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu.+ Musakhale achisoni ndipo musalire.” Ananena zimenezi chifukwa anthu onse ankalira pamene ankamvetsera mawu a mʼChilamulocho.
10 Nehemiya anati: “Pitani mukadye zinthu zabwino kwambiri,* mukamwe zokoma ndiponso mukagawire chakudya+ anthu amene alibe, chifukwa lero ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Musadzimvere chisoni, chifukwa chimwemwe chimene Yehova amapereka ndi malo anu achitetezo.”*
11 Alevi ankauza anthu onse kuti asachite phokoso. Ankanena kuti: “Khalani chete chifukwa lero ndi tsiku lopatulika, choncho musadzimvere chisoni.”
12 Ndiyeno anthu onse anapita kukadya, kukamwa, kukagawira ena chakudya ndiponso kukasangalala kwambiri+ chifukwa anamvetsa bwino mawu amene anawafotokozera.+
13 Pa tsiku lachiwiri, atsogoleri a mabanja a anthu onse, ansembe ndiponso Alevi, anasonkhana pamodzi pamaso pa Ezara wokopera Malemba,* kuti amvetse bwino mawu a mʼChilamulo.
14 Ndiyeno anapeza kuti mʼChilamulo chimene Yehova anawapatsa kudzera mwa Mose analembamo kuti Aisiraeli azikhala mʼmisasa pa nthawi yachikondwerero mʼmwezi wa 7.+
15 Analembamonso kuti azilengeza mofuula+ mʼmizinda yonse ndi ku Yerusalemu konse kuti: “Pitani kumapiri mukatenge nthambi za mitengo ya maolivi, nthambi za mitengo ya paini, nthambi za mitengo ya mchisu, mitengo ya kanjedza ndi nthambi za masamba ambiri za mitengo ina kuti mudzamangire misasa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.”
16 Choncho anthu anapita nʼkukatenga zinthu zimenezi ndipo anamangira misasa. Aliyense anamanga msasa pamwamba pa nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu woona,+ mʼbwalo lalikulu la Geti la Kumadzi+ ndiponso mʼbwalo lalikulu la Geti la Efuraimu.+
17 Choncho gulu lonse la anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo anamanga misasa nʼkukhala mʼmisasayo. Anthu anasangalala kwambiri+ chifukwa Aisiraeli anali asanachitepo zimenezi kuchokera mu nthawi ya Yoswa+ mwana wa Nuni, mpaka nthawi imeneyi.
18 Ndiyeno tsiku lililonse, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, ankawerenga mokweza buku la Chilamulo cha Mulungu woona.+ Anachita chikondwererochi masiku 7 ndipo pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera mogwirizana ndi Chilamulo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mlembi.”
^ Kapena kuti, “mlembi.”
^ Kapena kuti, “Zikhale momwemo!”
^ Kapena kuti, “mlembi.”
^ Kapena kuti, “Tirisata,” dzina la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zonona.”
^ Kapena kuti, “chimakupatsani mphamvu.”
^ Kapena kuti, “mlembi.”