Wolembedwa ndi Mateyu 25:1-46

  • CHIZINDIKIRO CHA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-46)

    • Fanizo la anamwali 10 (1-13)

    • Fanizo la matalente (14-30)

    • Nkhosa komanso mbuzi (31-46)

25  “Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi anamwali 10 amene anatenga nyale zawo+ nʼkupita kukachingamira mkwati.+ 2  Anamwali 5 anali opusa ndipo 5 anali ochenjera.*+ 3  Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta owonjezera. 4  Koma ochenjerawo anatenga mafuta owonjezera mʼmabotolo awo limodzi ndi nyale zawo. 5  Popeza mkwati anachedwa kubwera, onse anayamba kusinza kenako anagona. 6  Pakati pa usiku kunamveka mawu ofuula akuti: ‘Mkwati uja wafika! Tulukani mukamuchingamire.’ 7  Nthawi yomweyo anamwali onsewo anadzuka nʼkukonza nyale zawo.+ 8  Opusa aja anauza ochenjera kuti, ‘Tigawireniko mafuta anu, chifukwa nyale zathu zatsala pangʼono kuzima.’ 9  Ochenjerawo anayankha kuti: ‘Mwina satikwanira tikagawana ndi inu. Pitani kwa ogulitsa kuti mukagule anu.’ 10  Atanyamuka kupita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali atakonzeka aja analowa naye limodzi mʼnyumba imene munali phwando laukwati+ ndipo chitseko chinatsekedwa. 11  Pambuyo pake anamwali ena aja nawonso anafika nʼkunena kuti, ‘Ambuye, ambuye, titsegulireni!’+ 12  Iye anawayankha kuti, ‘Kunena zoona, sindikukudziwani.’ 13  Choncho pitirizani kukhala maso+ chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.+ 14  Chifukwa zili ngati munthu amene ankafuna kupita kudziko lina, ndipo anaitanitsa akapolo ake nʼkuwasungitsa chuma chake.+ 15  Woyamba anamupatsa ndalama zokwana matalente* 5, wachiwiri anamupatsa matalente awiri ndipo wachitatu anamupatsa talente imodzi. Aliyense anamupatsa mogwirizana ndi luso lake ndipo iye anapita kudziko lina. 16  Nthawi yomweyo amene analandira matalente 5 uja ananyamuka kukachita nawo malonda ndipo anapindula matalente enanso 5. 17  Chimodzimodzinso amene analandira matalente awiri uja, anapindula enanso awiri. 18  Koma kapolo amene analandira imodzi yokha uja anapita kukakumba pansi nʼkubisa ndalama* ya mbuye wakeyo. 19  Patapita nthawi yaitali, mbuye wa akapolowo anabwera nʼkuwerengerana nawo ndalama.+ 20  Choncho amene analandira matalente 5 uja anabwera ndi matalente ena owonjezera 5 nʼkunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente 5 koma onani, ndapindula matalente enanso 5.’+ 21  Mbuye wakeyo anamuyankha kuti: ‘Wachita bwino kwambiri, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupirika! Unakhulupirika pa zinthu zochepa, ndikuika kuti uziyangʼanira zinthu zambiri.+ Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.’+ 22  Kenako kunabwera kapolo amene analandira matalente awiri uja nʼkunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente awiri koma taonani, ndapindula matalente enanso awiri.’+ 23  Mbuye wake anamuyankha kuti: ‘Wachita bwino kwambiri, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupirika! Unakhulupirika pa zinthu zochepa, ndikuika kuti uziyangʼanira zinthu zambiri. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.’ 24  Pa mapeto pake kunabwera kapolo amene analandira talente imodzi uja, ndipo anati: ‘Ambuye, ndinkadziwa kuti inu ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese ndipo mumatuta tirigu kumene simunapete.+ 25  Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita kukabisa talente yanu ija pansi. Ndalama yanu iyi, landirani.’ 26  Mbuye wakeyo anayankha kuti: ‘Kapolo woipa ndi waulesi iwe! Ukuti unkadziwa kuti ineyo ndimakolola kumene sindinafese ndi kututa tirigu kumene sindinapete? 27  Ndiyetu zikanakhala bwino ukanasungitsa ndalama* zangazo kwa osunga ndalama, ndipo ine pobwera ndikanalandira ndalamazo limodzi ndi chiwongoladzanja chake. 28  Choncho mulandeni talenteyo nʼkuipereka kwa amene ali ndi matalente 10.+ 29  Chifukwa aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zinanso zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 30  Ponyani kapolo wopanda pake ameneyu kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’ 31  Mwana wa munthu+ akadzabwera mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo onse,+ adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero. 32  Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mofanana ndi mmene mʼbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. 33  Adzaika nkhosa+ kudzanja lake lamanja koma mbuzi adzaziika kudzanja lake lamanzere.+ 34  Kenako Mfumu idzauza amene ali kudzanja lake lamanja kuti: ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu Ufumu umene anakukonzerani kuchokera pachiyambi cha dziko lapansi.* 35  Chifukwa ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya. Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+ 36  Ndinali wamaliseche* koma inu munandiveka.+ Ndinadwala koma inu munandisamalira. Ndinali mʼndende koma inu munabwera kudzandiona.’+ 37  Ndiyeno olungamawo adzamuyankha kuti: ‘Ambuye, tinakuonani liti muli wanjala ife nʼkukudyetsani, kapena muli waludzu, ife nʼkukupatsani chakumwa?+ 38  Tinakuonani liti muli mlendo ife nʼkukulandirani bwino, kapena muli wamaliseche ife nʼkukuvekani? 39  Tinakuonani liti mukudwala kapena tinabwera liti kudzakuonani muli mʼndende?’ 40  Koma poyankha Mfumuyo idzawauza kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, nthawi iliyonse imene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aangʼono awa, munachitiranso ine.’+ 41  Kenako adzauza amene ali kumanzere kwake kuti, ‘Chokani pamaso panga+ anthu otembereredwa inu. Pitani kumoto wosatha+ umene anakolezera Mdyerekezi ndi angelo ake.+ 42  Chifukwa ndinamva njala koma inu simunandipatse chakudya. Ndinamva ludzu koma inu simunandipatse chakumwa. 43  Ndinali mlendo koma inu simunandilandire bwino. Ndinali wamaliseche koma inu simunandiveke. Ndinadwala komanso ndinali mʼndende koma inu simunandisamalire.’ 44  Iwonso adzayankha kuti: ‘Ambuye, tinakuonani liti muli ndi njala kapena muli ndi ludzu kapena muli mlendo kapena muli wamaliseche kapena mukudwala kapena muli mʼndende ife osakutumikirani?’ 45  Kenako iye adzawayankha kuti: ‘Ndithu ndikukuuzani, nthawi iliyonse imene simunachitire zimenezo mmodzi wa aangʼono awa, simunachitirenso ine.’+ 46  Anthu amenewa adzachoka kupita kuchiwonongeko chosatha,*+ koma olungama kumoyo wosatha.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anzeru.”
Talente imodzi ya Agiriki inali yofanana ndi makilogalamu 20.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndalama ya siliva.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndalama zasiliva.”
Apa akunena za ana a Adamu ndi Hava.
Kapena kuti, “wosavala mokwanira.”
Kapena kuti, “adzaphedwa.”