Salimo 65:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.
65 Inu Mulungu, tidzakutamandani mu Ziyoni,+Tidzakwaniritsa malonjezo athu kwa inu.+
2 Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+
3 Zolakwa zanga zandikulira,+Koma inu mumatikhululukira machimo athu.+
4 Wosangalala ndi munthu amene inu mwamusankha nʼkumubweretsa pafupi ndi inu,Kuti akhale mʼmabwalo anu.+
Tidzakhutira ndi zinthu zabwino zamʼnyumba yanu,+Kachisi wanu woyera.*+
5 Mudzatiyankha pochita zinthu zachilungamo zomwe ndi zochititsa mantha,+Inu Mulungu amene mumatipulumutsa.Anthu amene amakhala kumbali zonse za dziko lapansi amakudalirani+Kuphatikizapo amene amakhala kutali, kutsidya la nyanja.
6 Ndi mphamvu zanu, munakhazikitsa mapiri mʼmalo ake,Inu muli ndi mphamvu zochuluka.+
7 Mumachititsa kuti nyanja imene ikuchita mafunde ikhale bata.+Mumaletsa phokoso la mafunde ake komanso chipwirikiti cha mitundu ya anthu.+
8 Anthu okhala mʼmadera akutali adzachita mantha ndi zizindikiro zanu.+Mudzachititsa kuti anthu amene amakhala kumene dzuwa limatulukira mpaka kumene limalowera afuule mosangalala.
9 Inu mumasamalira dziko lapansi,Mumalichititsa kuti libale zipatso zambiri* komanso kuti likhale lachonde.+
Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wodzadza ndi madzi.Mumachititsa kuti dziko lapansi lipereke chakudya kwa anthu,+Umu ndi mmene dziko lapansi munalipangira.
10 Mumanyowetsa minda yake komanso kusalaza dothi limene lalimidwa,*Mumaifewetsa ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera zake.+
11 Chaka mumachiveka zinthu zabwino ndipo zimakhala ngati mwachiveka chisoti chachifumu.Munjira zanu mumakhala zinthu zambiri zabwino.*+
12 Mʼmalo odyetserako ziweto amʼchipululu muli msipu wambiri.*+Ndipo zitunda zavekedwa chisangalalo.+
13 Malo odyetserako ziweto adzaza ndi nkhosa,Ndipo mʼzigwa muli tirigu yekhayekha.+
Malo onsewa akufuula komanso kuimba mosangalala.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Malo oyera.”
^ Kapena kuti, “lisefukire ndi zokolola.”
^ Kapena kuti, “kusalaza mizere yake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Njira zanu zimakha mafuta.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mukukha mafuta.”