Salimo 34:1-22
Salimo la Davide, pa nthawi imene anachita zinthu ngati wamisala+ pamaso pa Abimeleki, moti anamuthamangitsa ndipo Davideyo anathawa.
א [Aleph]
34 Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.Sindidzasiya kumutamanda ndi pakamwa panga.
ב [Beth]
2 Monyadira, ndidzapereka ulemu kwa Yehova.*+Ofatsa adzamva ndipo adzasangalala.
ג [Gimel]
3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine,+Tiyeni tonse tikweze dzina lake.
ד [Daleth]
4 Ndinapemphera kwa Yehova ndipo iye anandiyankha.+
Anandipulumutsa ku zinthu zonse zimene zimandichititsa mantha.+
ה [He]
5 Amene anamukhulupirira anasangalala,Ndipo nkhope zawo sizinachite manyazi.
ז [Zayin]
6 Munthu wonyozekayu anaitana ndipo Yehova anamva.
Anamupulumutsa ku mavuto ake onse.+
ח [Heth]
7 Mngelo wa Yehova amamanga msasa kuzungulira anthu onse amene amaopa Mulungu,+Ndipo amawapulumutsa.+
ט [Teth]
8 Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.+Wosangalala ndi munthu amene amathawira kwa iye.
י [Yod]
9 Opani Yehova, inu oyera ake onse,Chifukwa onse amene amamuopa sasowa kanthu.+
כ [Kaph]
10 Ngakhale mikango yamphamvu* ingakhale ndi njala chifukwa chosowa chakudya.Koma anthu amene akufunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.+
ל [Lamed]
11 Bwerani kuno ana anga, ndimvetsereni.Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.+
מ [Mem]
12 Kodi ndi ndani pakati panu amene amakonda moyo,Ndipo angakonde atakhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+
נ [Nun]
13 Ndiyetu muteteze lilime lanu ku zinthu zoipa,+Komanso milomo yanu kuti isalankhule chinyengo.+
ס [Samekh]
14 Siyani kuchita zinthu zoipa ndipo muzichita zabwino.+Yesetsani kukhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+
ע [Ayin]
15 Maso a Yehova ali pa olungama,+Ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.+
פ [Pe]
16 Koma Yehova amakwiyira anthu ochita zoipa,Iye adzawawononga ndipo sadzakumbukiridwanso padziko lapansi.+
צ [Tsade]
17 Olungama anafuula ndipo Yehova anamva,+Iye anawapulumutsa mʼmavuto awo onse.+
ק [Qoph]
18 Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+Iye amapulumutsa anthu amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.*+
ר [Resh]
19 Mavuto* a munthu wolungama ndi ambiri,+Koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.+
ש [Shin]
20 Amateteza mafupa onse a munthu wolungamayo.Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+
ת [Taw]
21 Munthu woipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzafa.Anthu odana ndi munthu wolungama adzapezeka olakwa.
22 Yehova amawombola moyo wa atumiki ake.Palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeke wolakwa.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Ndidzadzitamandira mwa Yehova.”
^ Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”
^ Kapena kuti, “amene akhumudwa.”
^ Kapena kuti, “Masoka.”