Salimo 150:1-6
150 Tamandani Ya!*+
Tamandani Mulungu mʼmalo ake oyera.+
Mutamandeni mumlengalenga mmene mumasonyeza* mphamvu zake.+
2 Mutamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu.+
Mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wosaneneka.+
3 Mutamandeni poliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+
Mutamandeni ndi choimbira cha zingwe komanso zeze.+
4 Mutamandeni ndi maseche+ komanso gule wovina mozungulira.
Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe+ ndi chitoliro.+
5 Mutamandeni ndi zinganga za mawu osangalatsa.
Mutamandeni ndi zinganga za mawu amphamvu.+
6 Chamoyo chilichonse chitamande Ya.
Tamandani Ya!*+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “mmene mumachitira umboni za.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.