Wolembedwa ndi Luka 20:1-47
20 Tsiku lina akuphunzitsa anthu mʼkachisi komanso kulengeza uthenga wabwino, kunabwera ansembe aakulu, alembi limodzi ndi akulu
2 nʼkudzamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+
3 Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi ndipo mundiyankhe:
4 Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unachokera kumwamba kapena kwa anthu?”
5 Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’
6 Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala, chifukwa iwo amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane anali mneneri.”+
7 Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera.
8 Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”
9 Ndiyeno iye anayamba kuuza anthuwo fanizo ili: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndipo anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali ndithu.+
10 Ndiye nyengo ya zipatso itakwana, anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso zamʼmunda wa mpesawo. Koma alimiwo anamumenya nʼkumubweza chimanjamanja.+
11 Koma iye anawatumiziranso kapolo wina. Ameneyonso anamumenya nʼkumuchitira zachipongwe,* ndipo anamubweza chimanjamanja.
12 Anatumizanso wachitatu. Ameneyunso anamuvulaza nʼkumuponya kunja.
13 Zitatero mwiniwake wa munda wa mpesa uja anati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Chabwino, nditumiza mwana wanga wokondedwa.+ Mosakayikira mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’
14 Alimiwo atamuona anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa, uyu ndi amene adzalandire cholowa. Tiyeni timuphe kuti cholowacho chikhale chathu.’
15 Choncho anamutulutsa mʼmunda wa mpesawo nʼkumupha.+ Ndiye kodi mwiniwake wa munda wa mpesawo adzachita chiyani kwa alimiwo?
16 Iye adzabwera nʼkupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.”
Atamva zimenezi iwo anati: “Ayi zisatero ndithu!”
17 Koma iye anawayangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Paja malemba amanena kuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’*+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani?
18 Aliyense amene adzagwere pamwala umenewo adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, adzanyenyeka.”
19 Alembi ndi ansembe aakulu aja atazindikira kuti mufanizolo akunena za iwowo, anayesetsa kupeza mpata kuti amugwire ola lomwelo, koma ankaopa anthu.+
20 Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, nʼcholinga choti akamupezere zifukwa pa zimene angalankhule,+ kuti akamupereke kuboma ndi kwa bwanamkubwa.
21 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti zimene mumanena ndi kuphunzitsa ndi zolondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi.
22 Kodi nʼzololeka* kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”
23 Koma Yesu anazindikira ndale zawo ndipo anawauza kuti:
24 “Ndionetseni khobidi la dinari.* Kodi nkhope ndi mawu ali pamenepo ndi za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”
25 Iye anawauza kuti: “Choncho perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+
26 Iwo analephera kumutapa mʼkamwa pa zimene ananenazi pamaso pa anthu, koma anadabwa ndi yankho lake moti anangokhala chete kusowa chonena.
27 Koma Asaduki ena, amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+
28 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti, ‘Ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma sanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+
29 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira asanabereke mwana.
30 Wachiwirinso chimodzimodzi.
31 Kenako wachitatu anamukwatira. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja, onse anamwalira osasiya ana.
32 Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso.
33 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.”
34 Yesu anawayankha kuti: “Ana a mʼnthawi* ino amakwatira ndi kukwatiwa.
35 Koma amene aonedwa kuti ndi oyenerera kudzapeza moyo pa nthawi imeneyo nʼkudzaukitsidwa kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa.+
36 Komanso iwo sadzafanso, chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu pokhala ana a kuuka kwa akufa.
37 Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza munkhani ya chitsamba cha minga, pamene ananena kuti Yehova* ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+
38 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye* onsewa ndi amoyo.”+
39 Poyankha, ena mwa alembiwo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino.”
40 Ananena zimenezi chifukwa sanathenso kulimba mtima kuti amufunse funso lina ngakhale limodzi.
41 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+
42 Chifukwa Davideyo ananena mʼbuku la Masalimo kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja
43 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+
44 Choncho Davide anamutchula kuti Ambuye. Ndiye zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?”
45 Kenako anthu onse akumvetsera, iye anauza ophunzira akewo kuti:
46 “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo komanso amakonda kupatsidwa moni mʼmisika. Amakondanso kukhala mʼmipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso mʼmalo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo.+
47 Iwo amalanda chuma cha akazi* amasiye ndipo amapereka mapemphero ataliatali pofuna kudzionetsera.* Anthu amenewa adzalandira chilango chowawa kwambiri.”*
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “anamumenya nʼkumunyoza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”
^ Kapena kuti, “nʼzoyenera.”
^ Onani Zakumapeto B14.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “chifukwa iye amaona kuti.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “mʼmipando yabwino kwambiri.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Iwo amadya nyumba za akazi.”
^ Kapena kuti, “ataliatali mwachiphamaso.”
^ Kapena kuti, “chilango champhamvu.”