Wolembedwa ndi Luka 15:1-32

  • Fanizo la nkhosa yotayika (1-7)

  • Fanizo la khobidi lotayika (8-10)

  • Fanizo la mwana wolowerera (11-32)

15  Tsopano okhometsa msonkho onse komanso anthu ochimwa, ankabwera kwa Yesu kuti adzamumvetsere.+ 2  Ndiye Afarisi ndi alembi ankangʼungʼudza kuti: “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa nʼkumadya nawo limodzi.” 3  Choncho iye anawauza fanizo ili: 4  “Ndi ndani pakati panu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nʼkusowa, sangasiye nkhosa 99 zinazo mʼchipululu nʼkupita kukafunafuna imodzi imene yasowayo mpaka ataipeza?+ 5  Ndipo akaipeza amainyamula paphewa pake ndipo amasangalala. 6  Akafika kunyumba amasonkhanitsa anzake ndi anthu oyandikana naye nyumba nʼkuwauza kuti, ‘Sangalalani limodzi ndi ine, chifukwa ndapeza nkhosa yanga imene inasowa ija.’+ 7  Ndithu ndikukuuzani kuti, mofanana ndi zimenezi, kumwamba kudzakhala chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa+ kuposa cha anthu 99 olungama amene sakufunika kulapa. 8  Kapena ndi mayi uti amene ali ndi ndalama zokwana madalakima 10,* ndiye imodzi itamutayika, sangayatse nyale ndi kusesa mʼnyumba nʼkuifufuza mosamala mpaka ataipeza? 9  Ndipo akaipeza amasonkhanitsa anzake* komanso anthu oyandikana nawo nyumba nʼkuwauza kuti, ‘Sangalalani limodzi ndi ine, chifukwa ndapeza khobidi la dalakima* limene linanditayika lija.’ 10  Choncho ndikukuuzani kuti, mofanana ndi zimenezi, angelo a Mulungu amasangalala kwambiri chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa.”+ 11  Kenako ananena kuti: “Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. 12  Wamngʼono anapempha bambo ake kuti, ‘Bambo, mundipatsiretu cholowa changa pa chuma chanuchi.’ Choncho bambowo anagawa chuma chawocho kwa anawo. 13  Patangopita masiku owerengeka, mwana wamngʼono uja anasonkhanitsa zinthu zake zonse nʼkupita kudziko lina lakutali. Kumeneko anayamba kukhala moyo wotayilira ndipo anasakaza chuma chake chonse. 14  Atawononga chuma chake chonse, mʼdziko lonselo munagwa njala yaikulu ndipo iye anayamba kuvutika kwambiri. 15  Moti anapita kumakagwira ntchito kwa nzika ina yamʼdzikolo ndipo inamutumiza kubusa kwake kuti azikaweta nkhumba.+ 16  Iye anafika pomalakalaka chakudya chimene nkhumbazo zinkadya, koma palibe amene ankamupatsa kanthu. 17  Nzeru zitamubwerera ananena kuti, ‘Komatu aganyu ambiri a bambo anga ali ndi chakudya chochuluka, koma ine kuno ndikufa ndi njala! 18  Basi ndinyamuka ndizipita kwa bambo anga ndikawauze kuti: “Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu. 19  Si inenso woyenera kutchulidwa kuti mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.”’ 20  Choncho ananyamukadi nʼkupita kwa bambo ake. Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa ndi chifundo. Kenako anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa* mwachikondi. 21  Ndiyeno mwanayo anauza bambo akewo kuti, ‘Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu.+ Si inenso woyenera kutchulidwa kuti mwana wanu.’ 22  Koma bambowo anauza akapolo ake kuti, ‘Fulumirani, tengani mkanjo wabwino kwambiri uja mumuveke. Mumuvekenso mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi kwake. 23  Komanso mubweretse mwana wa ngʼombe wamphongo wonenepa, mumuphe ndipo tidye ndi kusangalala. 24  Chifukwa mwana wangayu anali wakufa koma tsopano wakhalanso ndi moyo,+ anatayika koma wapezeka.’ Choncho onse anayamba kusangalala. 25  Koma mwana wamkulu anali kumunda. Ndiyeno pamene ankabwerera nʼkuyandikira kunyumbako, anamva phokoso la nyimbo komanso anthu akuvina. 26  Choncho anaitana mmodzi wa antchito nʼkumufunsa chimene chinkachitika. 27  Iye anamuuza kuti, ‘Mngʼono wanu wabwera ndipo bambo anu amuphera mwana wa ngʼombe wonenepa, chifukwa amulandira ali bwinobwino.’* 28  Koma iye anakwiya kwambiri moti anakana kulowa mʼnyumbamo. Ndiyeno bambo akewo anatuluka nʼkuyamba kumuchonderera. 29  Poyankha iye anauza bambo akewo kuti, ‘Zaka zonsezi ine ndakhala ndikukugwirirani ntchito ngati kapolo ndipo sindinaphwanyepo malamulo anu nʼkamodzi komwe. Koma simunandipatseko ngakhale kamwana ka mbuzi kuti ndisangalale ndi anzanga. 30  Koma atangofika mwana wanuyu, amene anawononga* chuma chanu ndi mahule, mwamuphera mwana wa ngʼombe wamphongo wonenepa bwino.’ 31  Bambo akewo anamuuza kuti, ‘Mwana wanga, iwe wakhala nane nthawi zonse ndipo zinthu zonse zimene ine ndili nazo ndi zako. 32  Komatu tinangoyenera kusangalala ndi kukondwera, chifukwa mʼbale wakoyu anali wakufa koma panopa ali ndi moyo, anatayika koma panopa wapezeka.’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “azimayi ena omwe ndi anzake.”
Kapena kuti, “anamupsompsona.”
Kapena kuti, “ali wotetezeka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anadya.”