Wolembedwa ndi Luka 13:1-35

  • Lapani apo ayi mudzawonongedwa (1-5)

  • Fanizo la mtengo wa mkuyu wosabereka (6-9)

  • Mzimayi wopindika msana anachiritsidwa tsiku la Sabata (10-17)

  • Fanizo la kanjere ka mpiru komanso la zofufumitsa (18-21)

  • Pakufunika khama kuti tilowe pakhomo lalingʼono (22-30)

  • Herode ananenedwa kuti “nkhandwe” (31-33)

  • Yesu analirira Yerusalemu (34, 35)

13  Pa nthawiyo, ena mwa anthu amene anali pamenepo anamufotokozera za Agalileya amene magazi awo, Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo. 2  Iye anawayankha kuti: “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewo anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa chakuti zimenezo zinawachitikira? 3  Ayi ndithu. Choncho ndikukuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzawonongedwa mofanana ndi iwowo.+ 4  Nanga bwanji za anthu 18 aja, amene nsanja inawagwera ku Siloamu nʼkuwapha? Kodi mukuganiza kuti anali ochimwa kwambiri kuposa anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu? 5  Ayi ndithu. Choncho ndikukuuzani kuti, ngati simulapa, nonsenu mudzawonongedwa ngati mmene iwo anawonongedwera.” 6  Kenako anayamba kufotokoza fanizo ili: “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu mʼmunda wake wa mpesa, ndipo anapita kukafuna chipatso mumtengowo, koma sanapezemo chilichonse.+ 7  Ndiyeno anauza munthu wosamalira munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna nkhuyu mumtengowu, koma sindinapezemo ngakhale imodzi. Uduleni mtengo umenewu! Nʼchifukwa chiyani ukungowononga nthaka?’ 8  Wosamalira mundayo anayankha kuti, ‘Mbuyanga, bwanji muusiye chaka chino chokha. Ine ndikumba kuzungulira mtengowu nʼkuthirapo manyowa. 9  Ukadzabereka zipatso mʼtsogolo, zidzakhala bwino, koma ngati sudzabereka mudzaudule.’”+ 10  Tsopano ankaphunzitsa mʼsunagoge winawake pa Sabata. 11  Mmenemo munali mayi wina amene mzimu woipa* unamudwalitsa kwa zaka 18. Iye anali wopindika msana moti sankatha kuweramuka. 12  Yesu atamuona, analankhula naye nʼkumuuza kuti: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.”+ 13  Ndiyeno anaika manja ake pamayiyo, ndipo nthawi yomweyo anaweramuka nʼkuyamba kutamanda Mulungu. 14  Koma mtsogoleri wa sunagoge ataona zimenezi, anakwiya chifukwa Yesu anachiritsa munthu pa Sabata. Choncho anauza gulu la anthu kuti: “Pali masiku 6 amene tikuyenera kugwira ntchito.+ Muzibwera masiku amenewo kudzachiritsidwa, osati tsiku la Sabata.”+ 15  Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Achinyengo inu,+ kodi aliyense wa inu samasula ngʼombe yake kapena bulu wake mʼkhola pa Sabata nʼkupita naye kukamumwetsa madzi?+ 16  Kodi sikunali koyenera kuti mayi uyu, amenenso ndi mwana wa Abulahamu, amene Satana anamumanga kwa zaka 18, amasulidwe mʼmaunyolo amenewa tsiku la Sabata?” 17  Atanena zimenezi, onse amene ankamutsutsa anachita manyazi. Koma gulu lonse la anthu linayamba kusangalala chifukwa cha zodabwitsa zonse zimene iye anachita.+ 18  Choncho anapitiriza kunena kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, nanga ndingauyerekezere ndi chiyani? 19  Uli ngati kanjere ka mpiru* kamene munthu anakatenga nʼkukadzala mʼmunda wake. Kenako kanamera nʼkukhala mtengo, moti mbalame zamumlengalenga zinamanga zisa munthambi zake.”+ 20  Iye ananenanso kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu ndingauyerekezere ndi chiyani? 21  Uli ngati zofufumitsa zimene mayi wina anazitenga nʼkuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zazikulu zoyezera,* moti mtanda wonsewo unafufuma.”+ 22  Yesu anayenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Iye ankaphunzitsa nʼkumapitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 23  Ndiyeno munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi nʼzoona kuti anthu amene adzapulumuke ndi ochepa?” Iye anawauza kuti: 24  “Yesetsani mwamphamvu kuti mulowe pakhomo lalingʼono.+ Chifukwa ndithu ndikukuuzani, ambiri adzafunitsitsa kulowamo koma sadzatha. 25  Mwininyumba akadzanyamuka nʼkukiya chitseko, inu mudzaima panja nʼkumagogoda chitsekocho, ndipo mudzanena kuti, ‘Ambuye titsegulireni.’+ Koma iye adzakuyankhani kuti: ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera.’ 26  Ndiyeno mudzayamba kunena kuti, ‘Tinkadya ndi kumwa pamaso panu ndipo inu munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.’+ 27  Koma iye adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera. Chokani pamaso panga, inu nonse ochita zinthu zosalungama!’ 28  Kumeneko mudzalira ndi kukukuta mano mukadzaona Abulahamu, Isaki ndi Yakobo komanso aneneri onse ali mu Ufumu wa Mulungu, koma inuyo atakukankhirani kunja.+ 29  Komanso, anthu adzabwera kuchokera kumʼmawa, kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera ndipo adzakhala patebulo mu Ufumu wa Mulungu. 30  Ndithudi amene ali omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.”+ 31  Mu ola lomwelo kunafika Afarisi ena nʼkumuuza kuti: “Nyamukani muchoke kuno, chifukwa Herode akufuna kukuphani.” 32  Iye anawayankha kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe imeneyo kuti, ‘Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa, ndipo ndimaliza tsiku lachitatu.’ 33  Komabe ndiyenera kupitiriza ulendo wanga lero ndi mawa ndi tsiku linalo, chifukwa nʼkosayenera kuti mneneri amuphere kunja kwa Yerusalemu.+ 34  Yerusalemu, Yerusalemu, wopha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe.+ Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, ngati mmene nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake mʼmapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 35  Tsopano tamverani! Mulungu wachoka nʼkukusiyirani nyumba yanuyi.+ Ndithu ndikukuuzani, simudzandionanso mpaka pamene mudzanene kuti: ‘Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!’”*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mzimu wolumalitsa.”
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakangʼono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita 4 ndipo kamakhala ndi nthambi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “miyezo itatu ya seya.” Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.