Genesis 5:1-32

  • Kuyambira pa Adamu kudzafika pa Nowa (1-32)

    • Adamu anabereka ana aamuna ndi aakazi (4)

    • Inoki anayenda ndi Mulungu (21-24)

5  Ili ndi buku la mbiri ya Adamu. Pa tsiku* limene Mulungu analenga Adamu, anamupanga mʼchifaniziro cha Mulungu.+ 2  Anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.+ Pa tsiku limene anawalengalo,+ anawadalitsa nʼkuwatchula dzina lakuti Anthu.* 3  Adamu ali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamʼpatsa dzina lakuti Seti.+ 4  Adamu atabereka Seti, anakhala ndi moyo zaka 800, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 5  Choncho zaka zonse zimene Adamu anakhala ndi moyo zinakwana 930, kenako anamwalira.+ 6  Seti ali ndi zaka 105, anabereka Enosi.+ 7  Atabereka Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka 807, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 8  Choncho Seti anakhala ndi moyo zaka 912, kenako anamwalira. 9  Enosi ali ndi zaka 90, anabereka Kenani. 10  Atabereka Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka 815, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 11  Choncho Enosi anakhala ndi moyo zaka 905, kenako anamwalira. 12  Kenani ali ndi zaka 70, anabereka Mahalalele.+ 13  Atabereka Mahalalele, Kenani anakhala ndi moyo zaka 840, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14  Choncho Kenani anakhala ndi moyo zaka 910, kenako anamwalira. 15  Mahalalele ali ndi zaka 65, anabereka Yaredi.+ 16  Atabereka Yaredi, Mahalalele anakhala ndi moyo zaka 830, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 17  Choncho Mahalalele anakhala ndi moyo zaka 895, kenako anamwalira. 18  Yaredi ali ndi zaka 162, anabereka Inoki.+ 19  Atabereka Inoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka 800, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 20  Choncho Yaredi anakhala ndi moyo zaka 962, kenako anamwalira. 21  Inoki ali ndi zaka 65, anabereka Metusela.+ 22  Atabereka Metusela, Inoki anapitiriza kuyenda ndi Mulungu woona kwa zaka 300, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 23  Choncho Inoki anakhala ndi moyo zaka 365. 24  Inoki anayendabe ndi Mulungu woona.+ Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anamutenga.+ 25  Metusela ali ndi zaka 187, anabereka Lameki.+ 26  Atabereka Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka 782. Ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 27  Choncho Metusela anakhala ndi moyo zaka 969, kenako anamwalira. 28  Lameki ali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29  Mwanayo anamupatsa dzina lakuti Nowa,*+ ndipo anati: “Uyu ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yovuta komanso yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.”+ 30  Atabereka Nowa, Lameki anakhala ndi moyo zaka 595, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 31  Choncho Lameki anakhala ndi moyo zaka 777, kenako anamwalira. 32  Nowa atakwanitsa zaka 500 anabereka Semu,+ Hamu+ ndi Yafeti.+

Mawu a M'munsi

MʼBaibulo mawu akuti tsiku amanena za nthawi yotalika mosiyanasiyana, osati ya maola 24 yokha.
Kapena kuti, “mtundu wa anthu.”
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza kuti “Mpumulo; Kutonthoza.”