Genesis 22:1-24
22 Pambuyo pa zimenezi, Mulungu woona anamuyesa+ Abulahamu ndipo anati: “Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!”
2 Kenako Mulungu anamuuza kuti: “Tenga Isaki+ mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo,+ ndipo mupite ku Moriya.+ Kumeneko ukamupereke nsembe yopsereza paphiri limene ndidzakuuza.”
3 Choncho Abulahamu anadzuka mʼmawa kwambiri, nʼkumanga chishalo pabulu wake ndipo anatenga atumiki ake awiri limodzi ndi mwana wake Isaki. Komanso anawaza nkhuni zokawotchera nsembe. Atatero ananyamuka ulendo wopita kumalo amene Mulungu woona anamuuza.
4 Pa tsiku lachitatu, Abulahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali.
5 Kenako Abulahamu anauza atumiki akewo kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambira, tikupezani.”
6 Choncho Abulahamu anatenga nkhuni zokawotchera nsembe zija nʼkumusenzetsa Isaki mwana wake ndipo iye ananyamula moto komanso mpeni.* Kenako anapitira limodzi.
7 Ndiyeno Isaki analankhula ndi Abulahamu bambo ake kuti: “Bambo!” Abulahamu anayankha kuti: “Lankhula mwana wanga.” Choncho iye anafunsa kuti: “Moto ndi nkhuni nʼzimenezi, nanga nkhosa yokapereka nsembe yopsereza ili kuti?”
8 Abulahamu anayankha kuti: “Mwana wanga, Mulungu apereka nkhosa yoti tipereke nsembe yopsereza.”+ Choncho awiriwo anapitiriza ulendo wawo.
9 Kenako iwo anafika pamalo amene Mulungu woona anamuuza Abulahamu. Atafika pamalowo, iye anamanga guwa lansembe nʼkuyala nkhuni zija paguwapo. Atatero, anamanga Isaki mwana wakeyo manja ndi miyendo nʼkumugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni.+
10 Ndiyeno Abulahamu anatenga mpeni uja kuti aphe mwana wakeyo.+
11 Koma mngelo wa Yehova anamuitana kuchokera kumwamba kuti: “Abulahamu! Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!”
12 Ndiyeno mngeloyo anati: “Usamuvulaze mwanayo ndipo usamuchite chilichonse. Tsopano ndadziwa kuti umaopa Mulungu, chifukwa sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”+
13 Zitatero Abulahamu anakweza maso ake nʼkuona nkhosa yamphongo chapoteropo, nyanga zake zitakodwa mʼziyangoyango. Ndiyeno Abulahamu anakaitenga nʼkuipereka nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake.
14 Choncho Abulahamu anatchula malowo dzina lakuti Yehova-yire.* Nʼchifukwa chake mpaka lero pali mawu akuti: “Mʼphiri lake Yehova adzapereka zinthu zofunikira.”+
15 Ndiyeno mngelo wa Yehova anaitana Abulahamu kachiwiri kuchokera kumwamba,
16 nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndikulumbira pali dzina langa,+ kuti chifukwa cha zimene wachitazi, posakana kupereka mwana wako mmodzi yekhayo,+
17 ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbadwa* zako ngati nyenyezi zakumwamba komanso ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja.+ Ndipo mbadwa yako idzalanda mzinda* wa adani ake.+
18 Kudzera mwa mbadwa* yako,+ mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.’”+
19 Kenako Abulahamu anabwerera kwa atumiki ake aja nʼkunyamuka nawo limodzi kubwerera ku Beere-seba.+ Ndipo Abulahamu anapitiriza kukhala ku Beere-sebako.
20 Pambuyo pa zimenezi, uthenga unafika kwa Abulahamu wonena kuti: “Nayenso Milika waberekera mchimwene wako Nahori ana aamuna.+
21 Mwana wake woyamba ndi Uza, ndiye pali mchimwene wake Buza komanso Kemueli bambo ake a Aramu.
22 Palinso Kesede, Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betuele.”+
23 Betuele anabereka Rabeka.+ Ana 8 amenewa ndi amene Milika anaberekera Nahori mchimwene wake wa Abulahamu.
24 Mdzakazi* wa Nahori, dzina lake Reuma anamuberekeranso ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mpeni wophera nyama.”
^ Kutanthauza kuti, “Yehova Adzapereka,” kapena kuti, “Yehova Adziwa Chochita.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “geti la mzinda.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.