Ekisodo 38:1-31
38 Ndiyeno anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa a mthethe. Guwalo linali lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, mulitali linali mamita awiri* ndipo mulifupi linalinso mamita awiri. Kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 134.+
2 Anapanganso nyanga mʼmakona ake 4. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.* Atatero anakuta guwalo ndi kopa.*+
3 Kenako anapanga ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo. Anapanga ndowa, mafosholo, mbale zolowa, mafoloko aakulu ndi zopalira moto. Ziwiya zake zonse anazipanga ndi kopa.
4 Guwalo analipangiranso sefa wa zitsulo zakopa. Analowetsa sefayo chapakati pa guwa lansembe, mʼmunsi mwa mkombero.
5 Analipangiranso mphete 4 mʼmakona ake 4 kuti muzilowa ndodo zonyamulira. Mphetezo anazilumikiza pafupi ndi sefa wa zitsulo zakopa.
6 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe, ndipo anazikuta ndi kopa.
7 Ndodozo anazilowetsa mumphetezo mʼmbali mwa guwa kuti zikhale zonyamulira guwalo. Guwa limenelo analipanga ngati bokosi lamatabwa losatseka pansi.
8 Kenako anapanga beseni losambira lakopa+ ndi choikapo chake chakopa. Popanga zimenezi anagwiritsa ntchito magalasi odziyangʼanira* a azimayi amene ankatumikira pakhomo la chihema chokumanako.
9 Ndiyeno anapanga bwalo.+ Kumbali yakumʼmwera ya bwalolo anapangako mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri. Mpandawo unali mamita 45 mulitali mwake.+
10 Panali zipilala 20 ndi zitsulo 20 zakopa zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.
11 Kumbali yakumpoto, mpandawo unali mamita 45 mulitali mwake. Zipilala zake 20 ndi zitsulo 20 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.
12 Koma kumbali yakumadzulo, mpanda wa nsaluwo unali mamita 23 mulitali mwake. Kunali zipilala 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva.
13 Mulifupi mwake kumbali yakumʼmawa, kotulukira dzuwa, mpandawo unali mamita 23.
14 Kumbali imodzi ya khomo la bwalo, mpanda wa nsaluwo unali mamita 7. Kunali zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo.
15 Ndipo kumbali ina ya khomo la bwalolo, mpandawo unali mamita 7 mulitali mwake. Kunali zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo.
16 Nsalu zonse za mpanda wotchingira bwalo lonselo zinali za ulusi wopota wabwino kwambiri.
17 Zitsulo zokhazikapo zipilala zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu za mpanda ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. Pamwamba pa zipilalazo panali pokutidwa ndi siliva, ndipo zipilala zonse za bwalo zinali ndi tizitsulo tasiliva tolumikizira.+
18 Nsalu yotchinga pakhomo la bwalo anaiwomba ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Inali mamita 9 mulitali mwake, ndipo kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba inali mamita awiri, mofanana ndi nsalu zotchingira mpanda wa bwalo.+
19 Zipilala zake 4 ndi zitsulo 4 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilalazo tokolowekapo nsalu tinali tasiliva, ndipo pamwamba pa zipilalazo ndi tizitsulo tolumikizira anazikuta ndi siliva.
20 Zikhomo zonse za chihema ndi za bwalo lonse zinali zakopa.+
21 Mose analamula kuti awerengere zinthu zonse zimene anagwiritsa ntchito popanga chihema, kapena kuti chihema cha Umboni.+ Alevi ndi amene anachita zimenezi+ motsogoleredwa ndi Itamara+ mwana wa Aroni wansembe.
22 Bezaleli+ mwana wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda, anachita zonse zimene Yehova analamula Mose.
23 Iye anali ndi Oholiabu,+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani, mmisiri wa ntchito zosiyanasiyana, katswiri wodziwa kupeta komanso wodziwa kuwomba nsalu ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.
24 Golide yense amene anagwiritsidwa ntchito pa ntchito yonse yapamalo oyera, anali wochuluka mofanana ndi golide wa nsembe yoyendetsa uku ndi uku.+ Muyezo wake unali matalente* 29 ndi masekeli* 730 potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.*
25 Ndipo siliva wa anthu amene anawerengedwa mʼgulu la Isiraeli, anali matalente 100 ndi masekeli 1,775 potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.*
26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.* Anthu onse amene anawerengedwa analipo 603,550.+
27 Popanga zitsulo za malo oyera zokhazikapo mafelemu ndi zitsulo zokhazikapo zipilala za makatani anagwiritsa ntchito matalente 100. Popanga zitsulo 100 anagwiritsa ntchito matalente 100, talente imodzi anapangira chitsulo chimodzi.+
28 Masekeli 1,775 anawagwiritsa ntchito popangira tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi kukutira pamwamba pa zipilalazo. Atatero analumikiza zipilalazo.
29 Kopa amene anthu anapereka* anali matalente 70 ndi masekeli 2,400.
30 Kopa ameneyu anamugwiritsa ntchito popanga zitsulo zokhazikapo zipilala zapakhomo la chihema chokumanako, guwa lansembe lakopa, sefa wazitsulo wa guwalo ndi ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo.
31 Anapangiranso zitsulo zokhazikapo zipilala za mpanda wa bwalo lonse, zitsulo zokhazikapo zipilala zapakhomo la bwalolo, zikhomo zonse za chihema ndi zikhomo zonse za bwalo.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 5.” Onani Zakumapeto B14.
^ Kutanthauza kuti nyanga zimenezi sanazipangire padera nʼkuchita kuzilumikiza kuguwalo.
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Amenewa anali magalasi odziyangʼanira amene ankawapanga ndi chitsulo chimene ankachisalalitsa kwambiri kuti nkhope ya munthu izioneka.
^ Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
^ Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
^ Kapena kuti, “Kopa wa nsembe yoyendetsa uku ndi uku.”