Ekisodo 17:1-16
17 Gulu lonse la Aisiraeli linachoka kuchipululu cha Sini.+ Ulendowo anaugawa mʼzigawo, mogwirizana ndi mmene Yehova anawauzira,+ ndipo anamanga msasa ku Refidimu.+ Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa.
2 Ndiyeno anthu anayamba kukangana ndi Mose+ kuti: “Tipatse madzi timwe.” Koma Mose anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kuyesa Yehova?”+
3 Koma anthuwo anali ndi ludzu kwambiri ndipo anapitiriza kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa ku Iguputo kuti udzatiphe ndi ludzu limodzi ndi ana athu ndi ziweto zathu?”
4 Choncho Mose anafuulira Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pangʼono kundiponya miyala!”
5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tsogola ndipo utenge ena mwa akulu a Isiraeli komanso ndodo yako imene unamenya nayo mtsinje wa Nailo.+ Uitenge mʼdzanja lako ndipo uziyenda.
6 Tamvera! Ine ndidzatsogola nʼkukaima pathanthwe ku Horebe. Kumeneko ukamenye thanthwelo ndipo padzatuluka madzi amene anthu adzamwe.”+ Mose anachitadi zomwezo pamaso pa akulu a Isiraeli.
7 Choncho iye anatchula malowo kuti Masa*+ ndi Meriba,*+ chifukwa Aisiraeli anakangana ndi Mose komanso chifukwa chakuti anayesa Yehova+ kuti: “Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?”
8 Ndiyeno Aamaleki+ anabwera kudzamenyana ndi Isiraeli ku Refidimu.+
9 Zitatero Mose anauza Yoswa+ kuti: “Tisankhire amuna ndipo upite nawo kukamenyana ndi Aamaleki. Mawa ndikaima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu woona mʼdzanja langa.”
10 Yoswa anachitadi zimene Mose anamuuza,+ ndipo anamenyana ndi Aamaleki. Mose, Aroni ndi Hura+ anapita pamwamba pa phiri.
11 Ndiyeno Mose akakweza manja ake mʼmwamba, Aisiraeli ankapambana pankhondoyo, koma akangotsitsa manja ake, Aamaleki ankapambana.
12 Manja a Mose atatopa, anatenga mwala ndi kumuikira, ndipo anakhalapo. Aroni ndi Hura anagwira manja ake, wina dzanja lina winanso dzanja lina, moti manja ake anakhalabe okweza mpaka dzuwa kulowa.
13 Choncho Yoswa anagonjetsa Aamaleki ndi anthu amene anali kumbali yawo pogwiritsa ntchito lupanga.+
14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Lemba zimenezi mʼbuku kuti anthu azidzazikumbukira ndipo umuuze Yoswa kuti, ‘Ndidzafafaniziratu Aamaleki padziko lapansi ndipo sadzakumbukiridwa nʼkomwe.’”+
15 Choncho Mose anamanga guwa lansembe nʼkulipatsa dzina lakuti Yehova-nisi,*
16 ndipo anati: “Yehova adzamenya nkhondo ndi Aamaleki ku mibadwomibadwo+ chifukwa dzanja lawo laukira mpando wachifumu wa Ya.”+
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza, “Kuyesa; Mayesero.”
^ Kutanthauza, “Kukangana.”
^ Kutanthauza, “Yehova Ndi Mtengo Wanga Wachizindikiro.”