Deuteronomo 23:1-25
23 “Mwamuna amene anafulidwa pophwanya mavalo ake kapena amene anadulidwa maliseche asamalowe mumpingo wa Yehova.+
2 Mwana wapathengo asamalowe mumpingo wa Yehova.+ Ngakhale mpaka mʼbadwo wa 10, mbadwa zake zisamalowe mumpingo wa Yehova.
3 Mbadwa ya Amoni kapena Mowabu isamalowe mumpingo wa Yehova.+ Ngakhale mpaka mʼbadwo wa 10, mbadwa zawo zisadzalowe mumpingo wa Yehova mpaka kalekale,
4 chifukwa chakuti sanakuthandizeni pokupatsani chakudya ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ komanso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+
5 Koma Yehova Mulungu wanu anakana kumvera Balamu.+ Mʼmalomwake, Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+
6 Musamachite chilichonse powathandiza kuti azikhala mwamtendere komanso kuti zinthu ziwayendere bwino masiku onse a moyo wanu.+
7 Musamadane ndi mbadwa ya Edomu, chifukwa ndi mʼbale wanu.+
Musamadane ndi munthu wa ku Iguputo, chifukwa munali alendo mʼdziko lawo.+
8 Ana awo a mʼbadwo wachitatu angathe kulowa mumpingo wa Yehova.
9 Mukamanga msasa kuti mumenyane ndi adani anu, muzipewa chilichonse chodetsa.*+
10 Ngati mwamuna wadetsedwa chifukwa chotulutsa umuna usiku,+ azipita kunja kwa msasa ndipo asamalowenso mumsasamo.
11 Ndiyeno madzulo azisamba ndi madzi ndipo kenako angathe kubwerera kumsasa dzuwa likalowa.+
12 Muzikhala ndi malo apadera* kunja kwa msasa, kumene muzipita mukafuna kudzithandiza.
13 Pa zida zanu pazikhalanso chokumbira. Ndiyeno mukafuna kudzithandiza kunja kwa msasa, muzikumba dzenje ndi chokumbiracho ndipo mukamaliza muzikwirira zoipazo.
14 Chifukwa Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu+ kuti akupulumutseni ndi kupereka adani anu mʼmanja mwanu. Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu nʼkusiya kuyenda nanu limodzi.
15 Kapolo akathawa kwa mbuye wake nʼkubwera kwa inu, musamamubweze kwa mbuye wakeyo.
16 Iye azikhala pakati panu pamalo alionse amene angasankhe mu umodzi mwa mizinda yanu, kulikonse kumene wakonda. Ndipo musamamuzunze.+
17 Mwana wamkazi aliyense wa Chiisiraeli asakhale hule wapakachisi,+ ndiponso mwana wamwamuna aliyense wa Chiisiraeli asakhale hule wapakachisi.+
18 Musamabweretse malipiro a hule lalikazi kapena malipiro a hule lalimuna* mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kuti mukwaniritse lonjezo lililonse, chifukwa malipiro onsewo ndi onyansa kwa Yehova Mulungu wanu.
19 Mʼbale wanu musamamulipiritse chiwongoladzanja pa ndalama,+ chakudya kapena pa chilichonse chimene munthu angafunepo chiwongoladzanja.
20 Mlendo mungamulipiritse chiwongoladzanja,+ koma mʼbale wanu musamamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+
21 Mukalonjeza kanthu kwa Yehova Mulungu wanu+ musamachedwe kukwaniritsa zimene mwalonjezazo.+ Chifukwa Yehova Mulungu wanu adzafuna ndithu kuti mukwaniritse zimene mwalonjezazo. Mukapanda kutero mudzakhala kuti mwachimwa.+
22 Koma mukapanda kulonjeza, simudzachimwa.+
23 Muzisunga mawu a pakamwa panu+ ndipo muzikwaniritsa zimene munalonjeza ndi pakamwa panu monga nsembe yaufulu yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu.+
24 Mukalowa mʼmunda wa mpesa wa mnzanu mungathe kudya mphesa mmene mungathere kuti mukhute, koma musamaike zina mʼthumba lanu.+
25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mnzanu, mungathe kupulula ndi dzanja lanu tirigu amene wacha, koma musamamwete ndi chikwakwa tirigu wa mnzanu.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “choipa.”
^ Chimenechi ndi chimbudzi.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “galu.”