Kalata Yopita kwa Aheberi 8:1-13

  • Chihema chinkachitira chithunzi zinthu zakumwamba (1-6)

  • Kusiyana pakati pa pangano lakale ndi latsopano (7-13)

8  Pa zimene tikunenazi, mfundo yaikulu ndi yakuti: Tili ndi mkulu wa ansembe ngati ameneyu,+ ndipo iye wakhala kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka kumwamba.+ 2  Iye ndi mtumiki wamʼmalo oyerawo+ komanso mʼchihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova* osati munthu. 3  Mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka mphatso ndiponso nsembe. Choncho uyunso anafunika kukhala ndi chinachake choti apereke.+ 4  Iye akanakhalabe padziko lapansi sakanakhala wansembe,+ chifukwa pali kale amuna opereka mphatsozo malinga ndi Chilamulo. 5  Utumiki umene amuna amenewa akuchita uli ngati chifaniziro ndiponso chithunzi+ cha zinthu zakumwamba.+ Izi zikufanana ndi lamulo limene Mulungu anapatsa Mose atatsala pangʼono kumanga chihema. Lamulo lake linali lakuti: “Uonetsetse kuti wapanga zinthu zonse motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa mʼphiri.”+ 6  Koma Yesu walandira utumiki wapamwamba kwambiri, chifukwa iyenso ndi mkhalapakati+ wa pangano labwino kwambiri,+ limene lakhazikitsidwa mwalamulo pa malonjezo abwinonso.+ 7  Pangano loyamba lija likanakhala lopanda zolakwika, sipakanafunikanso pangano lachiwiri.+ 8  Chifukwa Mulungu akuona kuti anthu akulakwitsa zinazake choncho iye akunena kuti: “‘Taonani! Masiku akubwera pamene ndidzachita pangano latsopano ndi nyumba ya Isiraeli komanso ndi nyumba ya Yuda,’ akutero Yehova.* 9  ‘Koma silidzakhala pangano lofanana ndi limene ndinachita ndi makolo awo pa tsiku limene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse mʼdziko la Iguputo.+ Popeza sanapitirize kusunga pangano langalo, ndinasiya kuwasamalira,’ akutero Yehova.”* 10  “‘Pangano limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmaganizo mwawo ndiponso kuwalemba mʼmitima yawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,’+ akutero Yehova.* 11  ‘Munthu sadzaphunzitsanso nzika inzake kapena mʼbale wake kuti, “Mumʼdziwe Yehova!”* Chifukwa aliyense adzandidziwa kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. 12  Ine ndidzawachitira chifundo pa zochita zawo zosalungama, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.’”+ 13  Ponena kuti “pangano latsopano,” iye wachititsa kuti loyambalo lithe ntchito.+ Pangano limene latha ntchito ndipo likukalamba, ndiye kuti latsala pangʼono kufafanizika.+

Mawu a M'munsi