Kalata Yopita kwa Aheberi 7:1-28
7 Melekizedeki ameneyu anali mfumu ya mzinda wa Salemu komanso wansembe wa Mulungu Wamʼmwambamwamba, ndipo anachingamira Abulahamu pochokera kokapha mafumu nʼkumudalitsa.+
2 Abulahamu anamupatsa chakhumi cha zinthu zonse. Dzina lakeli limamasuliridwa kuti “Mfumu Yachilungamo” komanso mfumu ya Salemu, kutanthauza “Mfumu Yamtendere.”
3 Popeza analibe bambo, analibe mayi, analibe mzere wa makolo ndipo tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalira silikudziwika, koma anamuchititsa kuti afanane ndi Mwana wa Mulungu, iye ndi wansembe mpaka kalekale.+
4 Choncho mungaone kuti munthuyu anali wofunika kwambiri. Moti kholo lathu Abulahamu, anamupatsa chakhumi pa zinthu zabwino kwambiri zimene anatenga kunkhondo.+
5 Zoonadi mogwirizana ndi Chilamulo, ana aamuna a Levi+ amene amapatsidwa udindo wa unsembe, analamulidwa kuti azilandira zakhumi kuchokera kwa anthu.+ Anthu amenewa anali abale awo ngakhale kuti abale awowo anali mbadwa za Abulahamu.
6 Koma munthu ameneyu, yemwe sanachokere mumzere wobadwira wa Levi analandira chakhumi kuchokera kwa Abulahamu, ndipo anadalitsa Abulahamuyo amene analandira malonjezo kuchokera kwa Mulungu.+
7 Choncho palibe angatsutse kuti wamngʼono anadalitsidwa ndi wamkulu.
8 Alevi ankalandira zakhumi ndipo ndi anthu oti amafa. Koma munthu wina amene analandira zakhumi, Malemba amamuchitira umboni kuti ali moyo.+
9 Tikhozanso kunena kuti ngakhalenso Levi amene amalandira zakhumi anapereka zakhumi kudzera mwa Abulahamu.
10 Chifukwa Levi anali asanabadwe pamene kholo lake Abulahamu anakumana ndi Melekizedeki, koma anali woti adzakhala mbadwa ya Abulahamuyo.+
11 Kukhala ndi ansembe a fuko la Levi kunali mbali ya Chilamulo cha Mose chimene Aisiraeli anapatsidwa. Ndiye zikanakhala kuti ansembe a fuko la Levi angathandize anthu kukhala angwiro,+ kodi pakanafunikanso wansembe ngati Melekizedeki?+ Kodi sizikanakhala zokwanira kungokhala ndi wansembe ngati Aroni?
12 Popeza kuti unsembewo ukusinthidwa, ndiye kuti Chilamulonso chifunika kusintha.+
13 Munthu amene akufotokozedwa pamenepa ndi wa fuko lina ndipo palibe aliyense wa fuko limenelo amene anatumikirapo paguwa lansembe.+
14 Tonse tikudziwa kuti Ambuye wathu anachokera ku fuko la Yuda+ koma Mose sananenepo kuti ansembe adzachokera mu fuko limeneli.
15 Zimenezi zikumveka bwino tsopano chifukwa pabwera wansembe wina+ wofanana ndi Melekizedeki.+
16 Iyeyu wakhala wansembe, osati mogwirizana ndi malamulo, amene amadalira zinthu zapadziko lapansi, koma mogwirizana ndi mphamvu ya moyo umene sungawonongeke.+
17 Chifukwa Malemba anamuchitira umboni kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.”+
18 Choncho malamulo oyambawo akuchotsedwa chifukwa ndi operewera komanso osathandiza.+
19 Chilamulo sichinapangitse chilichonse kukhala changwiro.+ Koma chiyembekezo cha zinthu zabwino chimene anabweretsa,+ chomwe chikutithandiza kuyandikira Mulungu,+ chinachita zimenezi.
20 Komanso zimenezi sizinachitike popanda lumbiro.
21 (Chifukwa pali amuna ena amene akhala ansembe popanda lumbiro, koma ameneyu wakhala wansembe pochita kumulumbirira. Lumbiro limeneli ndi la amene ananena za wansembeyo kuti: “Yehova* walumbira kuti, ‘Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,’ ndipo sadzasintha maganizo.”)+
22 Mogwirizana ndi zimenezi, Yesu wakhala chikole cha pangano labwino kwambiri.+
23 Ndiponso pankafunika ansembe ambiri olowa mʼmalo+ chifukwa imfa inkachititsa kuti munthu asapitirize kukhala wansembe.
24 Koma popeza iye adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ palibe wansembe amene adzamulowe mʼmalo.
25 Choncho akhoza kupulumutsa anthu amene akupemphera kwa Mulungu mʼdzina lake, chifukwa iye sadzafa ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.+
26 Mkulu wa ansembe ngati ameneyu ndi wotiyeneradi chifukwa ndi wokhulupirika, wosalakwa, wosaipitsidwa,+ wosiyana ndi anthu ochimwa ndipo wakwezedwa pamwamba kwambiri.+
27 Mosiyana ndi akulu a ansembe ena, iye safunikira kupereka tsiku ndi tsiku nsembe+ za machimo ake choyamba, kenako za anthu ena.+ Zili choncho chifukwa iye anadzipereka kamodzi kokha kuti akhale nsembe yothandiza anthu mpaka kalekale.+
28 Chilamulo chimaika amuna okhala ndi zofooka kukhala akulu a ansembe.+ Koma mawu a lumbiro+ amene ananenedwa pambuyo pa Chilamulo anaika Mwana, amene anakhala wangwiro+ mpaka kalekale.
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto A5.