Kalata Yopita kwa Aheberi 1:1-14

  • Mulungu akulankhula kudzera mwa Mwana wake (1-4)

  • Mwana ndi wamkulu kuposa angelo (5-14)

1  Kalekale, Mulungu ankalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Anachita zimenezi kambirimbiri ndiponso mʼnjira zosiyanasiyana.+ 2  Kumapeto kwa masiku ano, iye walankhula ndi ife kudzera mwa Mwana wake,+ amene anamusankha kuti akhale wolandira zinthu zonse monga cholowa.+ Komanso kudzera mwa iyeyu, Mulungu anachititsa kuti pakhale nthawi* zosiyanasiyana.+ 3  Iye amasonyeza bwino ulemerero wa Mulungu+ ndipo ndi chithunzi chenicheni cha Mulunguyo.+ Komanso mawu ake amphamvu amathandiza kuti zinthu zikhalepobe. Ndipo atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala kudzanja lamanja la Wolemekezeka kumwamba.+ 4  Choncho iye wakhala woposa angelo,+ moti dzina limene walandira monga cholowa, ndi lapamwamba kwambiri kuposa lawo.+ 5  Mwachitsanzo, kodi Mulungu anauzapo mngelo uti kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala bambo ako”?+ Komanso kuti: “Ine ndidzakhala bambo ake ndipo iye adzakhala mwana wanga”?+ 6  Koma ponena za nthawi imene adzatumizenso Mwana wake woyamba kubadwayo+ padziko lapansi, iye akuti: “Angelo onse a Mulungu amugwadire.” 7  Ndiponso ponena za angelo, iye akuti: “Amachititsa kuti angelo ake akhale amphamvu* ndipo amachititsa atumiki ake+ kukhala ngati lawi la moto.”+ 8  Koma ponena za Mwana wake, iye akuti: “Mulungu ndi mpando wako wachifumu+ mpaka kalekale ndipo ndodo ya Ufumu wako, ndi ndodo yachilungamo. 9  Unkakonda chilungamo ndipo unkadana ndi kusamvera malamulo. Nʼchifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, anakudzoza+ ndi mafuta achisangalalo chachikulu kuposa mafumu anzako.”+ 10  Iye akunenanso kuti: “Ambuye, pachiyambipo munakhazikitsa maziko a dziko lapansi, ndipo kumwamba ndi ntchito ya manja anu. 11  Zinthu zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe. Mofanana ndi chovala, zonsezi zidzatha. 12  Mudzapindapinda zinthu zimenezi ngati mkanjo komanso ngati chovala ndipo zidzasinthidwa. Koma inu simudzasintha, ndipo mudzakhalapo mpaka kalekale.”+ 13  Koma kodi ndi mngelo uti amene anamuuzapo kuti: “Khala kudzanja langa lamanja, mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako”?+ 14  Angelo onse ndi mizimu yotumikira ena.*+ Mulungu amawatumiza kuti akatumikire omwe iye adzawapulumutse.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Amapanga angelo ake kukhala mizimu.”
Kapena kuti, “mizimu yochita utumiki wopatulika.”