Kalata Yachiwiri Yopita kwa Atesalonika 1:1-12

  • Moni (1, 2)

  • Chikhulupiriro cha Atesalonika chinkakulirakulira (3-5)

  • Anthu osamvera adzalandira chilango (6-10)

  • Ankapempherera mpingo (11, 12)

1  Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano* komanso Timoteyo+ ndipo ndikulembera mpingo wa Atesalonika, womwe ndi wogwirizana ndi Mulungu Atate wathu komanso Ambuye Yesu Khristu kuti: 2  Kukoma mtima kwakukulu komanso mtendere wochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu. 3  Tikuyenera kumathokoza Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Zimenezi nʼzoyenera chifukwa chikhulupiriro chanu chikukula kwambiri ndipo chikondi chimene aliyense amasonyeza kwa mnzake chikuwonjezereka.+ 4  Choncho ifeyo timanyadira+ tikamanena za inu ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chimene mumasonyeza mukamazunzidwa komanso kulimbana ndi mavuto* amene mukukumana nawo.*+ 5  Umenewu ndi umboni wakuti Mulungu amaweruza molungama ndipo chifukwa cha zimenezi mwaonedwa kuti ndinu oyenerera Ufumu wa Mulungu, umene mukuuvutikira.+ 6  Popeza Mulungu ndi wolungama, iye adzapereka chilango kwa amene amachititsa kuti muzizunzika.+ 7  Koma inu amene mukuvutika mudzapatsidwa mpumulo pamodzi ndi ife pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekere*+ kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu+ 8  mʼmoto walawilawi. Pa nthawi imeneyo adzabwezera chilango kwa anthu osadziwa Mulungu komanso kwa anthu amene samvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.+ 9  Anthu amenewa adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya+ ndipo adzachotsedwa pamaso pa Ambuye moti sadzaonanso mphamvu zake zaulemerero. 10  Zimenezi zidzachitika pa nthawi imene adzabwere kudzalandira ulemerero limodzi ndi oyera ake. Pa tsiku limenelo, onse amene anamukhulupirira adzamuyangʼanitsitsa mwachidwi, chifukwa munakhulupirira umboni umene tinapereka kwa inu. 11  Pa chifukwa chimenechi, timakupemphererani nthawi zonse kuti Mulungu wathu akuoneni kuti ndinu oyenereradi kuitanidwa ndi iye.+ Mulungu achite mokwanira zinthu zonse zabwino zimene akufuna kuchita ndi mphamvu zake, ndipo achititse kuti ntchito zanu zachikhulupiriro zikhale zopindulitsa. 12  Timakupemphererani kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezeke mwa inu komanso kuti inu mulemekezeke mwa iye, mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.

Mawu a M'munsi

Amene amadziwikanso kuti Sila.
Kapena kuti, “masautso.”
Kapena kuti, “mukuwapirira.”
Kapena kuti, “adzaululike.”