1 Samueli 14:1-52
14 Tsiku lina Yonatani+ mwana wa Sauli anauza mtumiki wake yemwe ankamunyamulira zida kuti: “Tiye tipite patsidyapo kwa asilikali a Afilisiti.” Koma bambo ake sanawauze.
2 Pa nthawiyi Sauli ankakhala kunja kwa mzinda wa Gibeya+ pansi pa mtengo wa makangaza* umene uli ku Migironi. Iye anali ndi anthu pafupifupi 600.+
3 (Ahiya ndi amene ankanyamula efodi.+ Iye anali mwana wa Ahitubu,+ mchimwene wa Ikabodi,+ mwana wa Pinihasi,+ mwana wa Eli+ yemwe anali wansembe wa Yehova ku Silo.)+ Koma anthu sanadziwe kuti Yonatani wachoka.
4 Pakati pa mipata imene Yonatani ankafuna kudutsa kuti akamenyane ndi asilikali a Afilisiti, panali matanthwe awiri. Lililonse linkaoneka ngati dzino ndipo lina linali mbali ina, lina mbali ina. Mayina a matanthwewo anali Bozezi ndi Sene.
5 Thanthwe limodzi linali kumpoto ngati chipilala ndipo linkayangʼana ku Mikimasi, pomwe lina linali kumʼmwera ndipo linkayangʼana ku Geba.+
6 Choncho Yonatani anauza womunyamulira zida uja kuti: “Tiye tipite kwa amuna osadulidwawa.+ Mwina Yehova adzatithandiza, chifukwa palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.”+
7 Womunyamulira zidayo anayankha kuti: “Chita zimene mtima wako ukufuna. Pita kulikonse kumene ungakonde ndipo ine ndikutsatira kulikonse kumene mtima wako ukufuna.”
8 Ndiyeno Yonatani anati: “Tiye tipite kwa anthuwa, ndipo tikachite zoti atione.
9 Iwo akakanena kuti, ‘Imani pompo, tikubwera komweko!’ ife tikaimadi ndipo sitikapitako.
10 Koma akakatiuza kuti, ‘Bwerani mudzamenyane nafe!’ ife tikapitedi chifukwa Yehova akawapereka mʼmanja mwathu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro chathu.”+
11 Ndipo iwo anachita zoti asilikali a Afilisiti awaone. Afilisitiwo atawaona anati: “Taonani Aheberi akutuluka mʼmaenje amene anabisala.”+
12 Asilikaliwo anauza Yonatani ndi mtumiki wakeyo kuti: “Bwerani tikukhaulitseni!”+ Nthawi yomweyo Yonatani anauza mtumiki wakeyo kuti: “Tiye, Yehova awapereka mʼmanja mwa Isiraeli.”+
13 Ndiyeno Yonatani anakwera matanthwe chokwawa ndipo mtumiki wake ankabwera mʼmbuyo mwake. Kenako Yonatani anayamba kupha Afilisitiwo ndipo mtumiki wake uja ankamalizitsa aliyense amene sanafe.
14 Nthawi yoyamba imene Yonatani ndi mtumiki wakeyo anamenyana ndi Afilisitiwo, anapha anthu pafupifupi 20 pamalo ochepa kwambiri.
15 Zitatero, asilikali onse amene anali pamalowo komanso amene anali kutchire mumsasa anayamba kuchita mantha. Nawonso asilikali amene ankalanda katundu+ anayamba kuchita mantha. Nthaka inayamba kugwedezeka ndipo Mulungu anachititsa kuti Afilisiti achite mantha.
16 Alonda a Sauli ku Gibeya+ wa ku Benjamini anaona kuti paliponse mumsasamo pali chipwirikiti.+
17 Sauli anauza anthu amene anali naye kuti: “Werengani anthu kuti muone amene wachoka.” Atawerenga anthuwo, anapeza kuti Yonatani ndi womunyamulira zida palibe.
18 Zitatero Sauli anauza Ahiya+ kuti: “Bweretsa kuno Likasa la Mulungu woona!” (Pa nthawiyi nʼkuti Likasa la Mulungu woona lili ndi Aisiraeli.)
19 Pa nthawi imene Sauli ankalankhula ndi wansembe, chipwirikiti chinkawonjezeka kwambiri mumsasa wa Afilisiti. Kenako Sauli anauza wansembeyo kuti: “Basi, siya zimene ukuchitazo.”
20 Choncho Sauli ndi anthu onse amene anali naye anasonkhana nʼkupita kukamenyana ndi Afilisiti. Atafika kumeneko anapeza kuti Afilisiti akumenyana okhaokha ndi malupanga, moti kunali chisokonezo chosaneneka.
21 Komanso Aheberi amene poyamba anagwirizana ndi Afilisiti, ndipo anapita kukakhala mumsasa wa Afilisiti, anachoka nʼkupita kumbali ya Aisiraeli amene anali ndi Sauli ndi Yonatani.
22 Amuna onse a Isiraeli amene anabisala+ mʼdera lamapiri la Efuraimu anamva kuti Afilisiti akuthawa, choncho nawonso anayamba kuthamangitsa Afilisitiwo.
23 Pa tsikuli Yehova anapulumutsa Aisiraeli,+ ndipo nkhondoyo inapitirira mpaka ku Beti-aveni.+
24 Koma amuna a Isiraeli anatopa kwambiri pa tsikuli chifukwa Sauli analumbirira anthuwo kuti: “Munthu aliyense amene angadye chakudya* chilichonse dzuwa lisanalowe, komanso ndisanabwezere adani anga, akhale wotembereredwa.” Choncho panalibe aliyense amene anadya chilichonse.+
25 Ndiyeno anthuwo anafika kunkhalango ndipo mʼnkhalangomo munali uchi wambiri.
26 Anthuwo anaona uchi ukukha. Koma palibe amene anadya chifukwa ankaopa lumbiro lija.
27 Koma Yonatani sanamve pamene bambo ake ankalumbirira anthu,+ moti anagwiritsa ntchito ndodo yake kutenga uchi pangʼono pachisa. Kenako anadya uchiwo ndipo atatero, anayera mʼmaso.
28 Ndiyeno munthu wina anamuuza kuti: “Bambo ako alumbirira anthu mwamphamvu kuti, ‘Munthu aliyense amene adye chakudya lero ndi wotembereredwa.’+ Nʼchifukwa chake anthuwa atopa kwambiri.”
29 Yonatani anayankha kuti: “Bambo anga achititsa kuti anthu avutike kwambiri. Taonani mmene maso anga ayerera nditangolawa uchi pangʼono.
30 Ndiye kuli bwanji anthu akanadya momasuka+ zimene atenga atagonjetsa adani awo? Bwenzi titapha Afilisiti ambiri kuposa pamenepa.”
31 Pa tsikuli iwo anapitiriza kupha Afilisiti kuyambira ku Mikimasi mpaka ku Aijaloni+ ndipo anthu anatopa kwambiri.
32 Zitatero, anthuwo anayamba kuthamangira zinthu za adani awowo mosusuka ndipo anatenga nkhosa, ngʼombe ndi ana a ngʼombe. Ankaziphera pansi ndipo ankadya nyamayo pamodzi ndi magazi ake.+
33 Ndiyeno anthu ena anauza Sauli kuti: “Anthutu akuchimwira Yehova. Akudya nyama pamodzi ndi magazi ake.”+ Iye anati: “Mwachita zinthu mopanda chikhulupiriro. Gubuduzani chimwala mubwere nacho kuno mwamsanga.”
34 Kenako Sauli anati: “Pitani mukauze anthu kuti, ‘Aliyense abweretse ngʼombe yake yamphongo ndi nkhosa ndipo adzaziphere pano kenako nʼkudya. Musachimwire Yehova podya nyama pamodzi ndi magazi ake.’”+ Choncho usiku umenewo, aliyense anabweretsa ngʼombe yake yamphongo nʼkuiphera pamenepo.
35 Ndiyeno Sauli anamangira Yehova guwa lansembe.+ Limeneli linali guwa lake loyamba kumangira Yehova.
36 Kenako Sauli anati: “Tiyeni tipite kwa Afilisiti usiku kukamenyana nawo ndipo tikalande zinthu zawo mpaka mʼmawa. Tisakasiye munthu aliyense wamoyo.” Anthuwo anayankha kuti: “Chitani chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino.” Ndiyeno wansembe anati: “Tiyeni tifunse Mulungu woona pamalo omwe ano.”+
37 Kenako Sauli anafunsa Mulungu kuti: “Kodi ndipite kwa Afilisiti?+ Kodi muwapereka mʼmanja mwa Aisiraeli?” Koma pa tsikuli Mulungu sanamuyankhe.
38 Choncho Sauli anati: “Atsogoleri nonse a anthu bwerani kuno kuti tidziwe tchimo limene lachitika lero.
39 Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, amene anapulumutsa Aisiraeli, yemwe wachita tchimoli ayenera kufa, ngakhale atakhala Yonatani mwana wanga.” Koma palibe aliyense amene anamuyankha.
40 Ndiyeno Sauli anauza Aisiraeli onse kuti: “Inuyo mukhale kumbali ina, ndipo ine ndi mwana wanga Yonatani tikhalanso ku mbali ina.” Anthuwo anauza Sauli kuti: “Chitani zimene mukuona kuti nʼzabwino.”
41 Ndiyeno Sauli anauza Yehova kuti: “Inu Mulungu wa Isiraeli, tiyankheni kudzera mwa Tumimu!”+ Atatero, Yonatani ndi Sauli anasankhidwa ndipo anthuwo anaoneka kuti alibe mlandu.
42 Kenako Sauli anati: “Chitani maere+ pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga.” Zitatero, maerewo anagwera Yonatani.
43 Sauli anafunsa Yonatani kuti: “Ndiuze, wachita chiyani?” Yonatani anayankha kuti: “Ndinalawa uchi pangʼono kunsonga ya ndodo imene ndatengayi.+ Ndiye ndine ndili pano. Mukhoza kundipha!”
44 Zitatero Sauli anati: “Mulungu andilange mowirikiza ngati suufa Yonatani.”+
45 Koma anthu anauza Sauli kuti: “Kodi Yonatani amene wapulumutsa+ Aisiraeli chonchi afe? Sizitheka zimenezo! Tikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, ngakhale tsitsi limodzi la mʼmutu wake siligwa pansi, chifukwa zimene wachita lerozi wathandizidwa ndi Mulungu.”+ Ndi mawu amenewa anthuwo anapulumutsa* Yonatani moti sanaphedwe.
46 Choncho Sauli anasiya kutsatira Afilisiti ndipo Afilisiti anabwerera kwawo.
47 Sauli analimbitsa ufumu wake mu Isiraeli ndipo anamenyana ndi adani ake mʼmadera onse. Anamenyana ndi Amowabu,+ Aamoni,+ Aedomu,+ mafumu a Zoba+ ndi Afilisiti.+ Kulikonse kumene ankapita ankagonjetsa adani akewo.
48 Iye ankamenya nkhondo molimba mtima ndipo anagonjetsa Aamaleki+ nʼkupulumutsa Aisiraeli kwa adani awowo.
49 Ana aamuna a Sauli anali Yonatani, Isivi ndi Malikisuwa.+ Iye analinso ndi ana aakazi awiri. Wamkulu dzina lake anali Merabu+ pamene wamngʼono anali Mikala.+
50 Mkazi wa Sauli dzina lake anali Ahinowamu, mwana wa Ahimazi. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Abineri+ mwana wa Nera, mchimwene wawo wa bambo ake a Sauli.
51 Bambo ake a Sauli anali Kisi,+ ndipo Nera+ bambo ake a Abineri, anali mwana wa Abiyeli.
52 Sauli ankamenyana kwambiri ndi Afilisiti mʼmasiku onse a moyo wake.+ Ndipo Sauli ankati akaona munthu aliyense wamphamvu kapena wolimba mtima, ankamutenga kuti akhale msilikali wake.+
Mawu a M'munsi
^ “Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anawombola.”