1 Mafumu 18:1-46
18 Patapita nthawi, mʼchaka chachitatu,+ Eliya anamva mawu a Yehova akuti: “Pita ukaonekere kwa Ahabu, chifukwa ndikufuna kubweretsa mvula mʼdzikoli.”+
2 Choncho Eliya anapita kukaonekera kwa Ahabu. Pa nthawiyi nʼkuti njala itafika poipa kwambiri+ ku Samariya.
3 Ahabu anaitana Obadiya, yemwe anali woyangʼanira banja la Ahabuyo. (Obadiya anali munthu woopa Yehova kwambiri.
4 Ndipo pamene Yezebeli+ ankapha aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri 100 nʼkuwagawa mʼmagulu awiri, gulu lililonse aneneri 50. Atatero anakawabisa kuphanga nʼkumawapatsa chakudya ndi madzi.)
5 Ndiyeno Ahabu anauza Obadiya kuti: “Pita mʼdzikoli, ukayendere akasupe onse a madzi ndi zigwa* zonse. Mwina tikhoza kupeza udzu wobiriwira woti tizidyetsa mahatchi ndi nyulu,* kuti ziweto zathuzi zisafe zonse.”
6 Choncho anagawana kopita. Ahabu analowera mbali ina ndipo Obadiya analowera mbali ina.
7 Obadiya akuyenda, anangoona Eliya akubwera kudzakumana naye. Nthawi yomweyo anamuzindikira ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake kufika pansi. Kenako ananena kuti: “Kodi ndinu mbuyanga Eliya?”+
8 Iye anamuyankha kuti: “Inde ndi ineyo. Pita ukauze abwana ako kuti, ‘Eliya wabwera.’”
9 Koma Obadiya anati: “Kodi ine mtumiki wanu ndalakwa chiyani kuti mundipereke kwa Ahabu kuti andiphe?
10 Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wanu wamoyo, palibe mtundu kapena ufumu kumene abwana anga sanatumizeko anthu kuti akakufufuzeni. Akanena kuti, ‘Kuno kulibe,’ ankauza ufumuwo ndiponso mtunduwo kuti ulumbire kuti walepheradi kukupezani.+
11 Ndiye mukundiuza kuti, ‘Pita ukauze abwana ako kuti: “Eliya wabwera”’?
12 Tikasiyana pano, mzimu wa Yehova ubwera nʼkukutengani+ kupita nanu kumalo amene ine sindingawadziwe. Ndiye ndikakauza Ahabu koma iyeyo osakupezani, adzandipha ndithu. Komatu ine mtumiki wanu ndakhala ndikuopa Yehova kuyambira ndili mwana.
13 Kodi inu mbuye wanga simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova? Ndinabisa aneneri 100 a Yehova mʼphanga. Ndinawagawa mʼmagulu awiri a aneneri 50 gulu lililonse ndipo ndinkawapatsa chakudya ndi madzi.+
14 Ndiye pano mukunena kuti, ‘Pita, ukauze abwana ako kuti: “Eliya wabwera”’? Ndithu akandipha.”
15 Koma Eliya anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wamoyo amene ndimamʼtumikira, lero ndionekera kwa Ahabu.”
16 Choncho Obadiya anapita kwa Ahabu kukamuuza zimenezi ndipo Ahabuyo anapita kukakumana ndi Eliya.
17 Ahabu atangoona Eliya, anati: “Kodi ndiwe eti? Iwe ndi amene wabweretsa mavuto ambiri mu Isiraeli.”
18 Eliya anayankha kuti: “Ine sindinabweretse mavuto mu Isiraeli, koma inuyo ndi nyumba ya bambo anu. Chifukwa mwasiya kutsatira malamulo a Yehova nʼkuyamba kutsatira Abaala.+
19 Tsopano sonkhanitsani Aisiraeli onse kuti ndikakumane nawo paphiri la Karimeli.+ Musonkhanitsenso aneneri 450 a Baala ndi aneneri 400 a mzati wopatulika,*+ amene amadya patebulo la Yezebeli.”
20 Choncho Ahabu anatumiza uthenga kwa Aisiraeli onse nʼkusonkhanitsanso aneneri paphiri la Karimeli.
21 Kenako Eliya anayandikira anthu onsewo nʼkunena kuti: “Kodi mukayikakayika mpaka liti?+ Ngati Yehova ali Mulungu woona mʼtsatireni,+ koma ngati Mulungu woona ndi Baala tsatirani ameneyo.” Koma anthuwo sanamuyankhe chilichonse.
22 Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Ndilipo ndekha mneneri wa Yehova amene watsala+ koma aneneri a Baala alipo 450.
23 Iwowo apeze ngʼombe zamphongo ziwiri zingʼonozingʼono. Asankhepo ngʼombe imodzi nʼkuiduladula. Ndiyeno aiike pankhuni koma asayatsepo moto. Ineyo ndikonza ngʼombe inayo nʼkuiika pankhuni, ndipo nanenso sindiyatsapo moto.
24 Kenako muitane dzina la mulungu wanu.+ Inenso ndiitana dzina la Yehova, ndipo Mulungu amene ayankhe potumiza moto asonyeza kuti ndi Mulungu woona.”+ Anthu onsewo atamva zimenezi anayankha kuti: “Zili bwino.”
25 Eliya anauza aneneri a Baala kuti: “Yambani ndinu kusankha ngʼombe imodzi nʼkuikonza chifukwa mulipo ambiri. Kenako muitane dzina la mulungu wanu koma musayatse moto.”
26 Choncho anatenga ngʼombe yaingʼono imene anapatsidwa nʼkuikonza ndipo kenako anayamba kuitana dzina la Baala kuyambira mʼmawa mpaka masana. Ankaitana kuti: “Inu a Baala, tiyankheni!” Koma sipanamveke mawu alionse ndipo palibe anayankha.+ Iwo anapitiriza kudumphadumpha uku akuzungulira guwa lansembe limene anamanga.
27 Pofika masana, Eliya anayamba kuwaseka nʼkumanena kuti: “Muitaneni mokuwa kwambiri chifukwa iye ndi mulungu.+ Mwina akuganizira zinazake kapena wapita kuchimbudzi.* Mwinanso wagona ndipo akufunika kumudzutsa.”
28 Iwo anayamba kuitana mokuwa kwambiri nʼkumadzichekacheka ndi mipeni ndi mikondo ingʼonoingʼono mogwirizana ndi mwambo wawo, mpaka magazi anayamba kuyenderera pamatupi awo.
29 Iwo anapitiriza kuchita ngati amisala* mpaka dzuwa linapendeka. Anapitirizabe mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo. Koma sipanamveke mawu alionse ndiponso palibe amene anayankha kapena kuwamvera.+
30 Patapita nthawi, Eliya anauza anthu onsewo kuti: “Bwerani pafupi.” Anthu onsewo anamuyandikira. Kenako iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linagumuka.+
31 Eliya anatenga miyala 12 mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a ana a Yakobo, yemwe Yehova anamuuza kuti: “Dzina lako lidzakhala Isiraeli.”+
32 Eliya anagwiritsa ntchito miyalayo nʼkumanga guwa lansembe+ kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. Kenako anakumba ngalande kuzungulira guwa lansembe lonselo. Ngalandeyo kukula kwake inali ngati malo amene angafesepo mbewu zokwana miyezo iwiri ya seya.*
33 Atatero anayalapo nkhuni ndipo anaduladula ngʼombe yaingʼono yamphongo ija nʼkuiika pamwamba pa nkhunizo.+ Kenako anati: “Tungani madzi odzaza mitsuko 4 ikuluikulu ndipo muwathire pansembe yopserezayo ndiponso pankhunizo.”
34 Atatero anati: “Thirani madzi ena.” Anthuwo anathiradi. Anawauzanso kuti: “Thiraninso kachitatu.” Choncho anthuwo anathiranso kachitatu.
35 Madziwo anayenderera pansi ponse pa guwa lansembelo. Iye anathiranso madzi mʼngalande muja mpaka kudzaza.
36 Ndiyeno pa nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo,+ mneneri Eliya anayandikira guwa lansembelo nʼkunena kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Isiraeli, lero zidziwike kuti inu ndinu Mulungu mu Isiraeli ndiponso kuti ine ndine mtumiki wanu, komanso kuti ndachita zonsezi potsatira mawu anu.+
37 Ndiyankheni Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe kuti inu Yehova ndinu Mulungu woona ndiponso kuti mukubweza mitima yawo kuti abwerere kwa inu.”+
38 Atatero, moto wa Yehova unatsika nʼkutentha nsembe yopsereza ija,+ nkhuni, miyala ndi fumbi lomwe. Unaumitsanso madzi amene anali mʼngalande aja.+
39 Anthu onsewo ataona zimenezo, nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi, ndipo ananena kuti: “Mulungu woona ndi Yehova! Mulungu woona ndi Yehova!”
40 Ndiyeno Eliya anauza anthuwo kuti: “Gwirani aneneri a Baala! Muonetsetse kuti pasapezeke wothawa!” Nthawi yomweyo anawagwira ndipo Eliya anatsetserekera nawo kumtsinje* wa Kisoni+ nʼkukawapha kumeneko.+
41 Kenako Eliya anauza Ahabu kuti: “Pitani mukadye ndi kumwa, chifukwa kukumveka mkokomo wa chimvula.”+
42 Ahabu anapitadi kukadya ndiponso kukamwa. Koma Eliya anapita pamwamba pa phiri la Karimeli ndipo anagwada nʼkuika nkhope yake pakati pa mawondo ake.+
43 Kenako anauza mtumiki wake kuti: “Pita ukayangʼane mbali yakunyanja.” Mtumikiyo anapita nʼkukayangʼanadi, ndiyeno anati: “Kulibe kalikonse.” Koma Eliya anamubweza nʼkumuuza kuti, “Pita ukayangʼanenso.” Anachita zimenezi mpaka maulendo 7.
44 Pa ulendo wa 7 mtumikiyo anati: “Ndaona kamtambo kakangʼono ngati dzanja la munthu ndipo kakukwera mʼmwamba kuchokera mʼnyanja.” Ndiyeno Eliya anauza mtumiki wakeyo kuti: “Pita ukauze Ahabu kuti, ‘Mangirirani mahatchi kugaleta ndipo munyamuke muzipita kuti chimvula chisakutsekerezeni.’”
45 Pa nthawiyi kumwamba kunachita mdima wa mitambo ndipo kunja kunayamba kuwomba mphepo. Kenako kunayamba kugwa chimvula chambiri.+ Ahabu anapitiriza ulendo wake pagaleta wopita ku Yezereeli.+
46 Koma dzanja la Yehova linapatsa Eliya mphamvu, moti anakokera chovala chake nʼkuchimanga mʼchiuno ndipo anayamba kuthamanga nʼkupitirira Ahabu mpaka kukafika ku Yezereeli.
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ “Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “kapena wachokapo.”
^ Kapena kuti, “kuchita ngati aneneri.”
^ Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “kuchigwa.”