Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 12:1-31
12 Tsopano abale, ponena za mphatso zauzimu,+ sindikufuna kuti mukhale osadziwa.
2 Mukudziwa kuti musanakhale okhulupirira,* munkatsogoleredwa ndiponso kusocheretsedwa ndi mafano osalankhula.+
3 Koma tsopano ndikufuna mudziwe kuti palibe munthu amene mzimu wa Mulungu ukumutsogolera yemwe anganene kuti: “Yesu ndi wotembereredwa!” Palibenso amene anganene kuti: “Yesu ndi Ambuye!” popanda kutsogoleredwa ndi mzimu woyera.+
4 Pali mphatso zosiyanasiyana, koma mzimu ndi umodzi.+
5 Ndipo pali mautumiki osiyanasiyana,+ koma Ambuye ndi mmodzi.
6 Ntchito ziliponso zosiyanasiyana, koma pali Mulungu mmodzi amene amapereka mphamvu yogwirira ntchitozo kwa munthu aliyense.+
7 Koma thandizo la mzimu woyera limaonekera kwa munthu aliyense, ndipo Mulungu amapereka mzimuwo nʼcholinga choti munthuyo azithandiza ena.+
8 Mwachitsanzo, mzimu umathandiza wina kulankhula mawu anzeru, ndipo mzimu womwewo umathandiza munthu wina kulankhula mawu ozindikira.
9 Mzimu womwewo umathandiza munthu wina kukhala ndi chikhulupiriro,+ pomwe wina umamuthandiza kukhala ndi mphatso yochiritsa,+
10 wina umamupatsa mphatso yochita ntchito zamphamvu,+ wina kunenera, wina kuzindikira mawu ouziridwa,+ wina kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana*+ ndiponso wina kumasulira zilankhulo.+
11 Koma zonsezi zimatheka ndi mzimu womwewo, ndipo munthu aliyense amapatsidwa mphatsozi motsogoleredwa ndi mzimuwo.
12 Thupi ndi limodzi, koma lili ndi ziwalo zambiri ndipo ziwalo zonse za thupi, ngakhale kuti nʼzambiri, zimapanga thupi limodzi.+ Ndi mmenenso zilili ndi Khristu.
13 Tonsefe tinabatizidwa ndi mzimu umodzi kuti tikhale thupi limodzi. Kaya ndife Ayuda kapena Agiriki, akapolo kapena anthu aufulu, tonsefe tinalandira* mzimu umodzi.
14 Thupi silikhala ndi chiwalo chimodzi, koma zambiri.+
15 Ngati phazi linganene kuti: “Popeza si ine dzanja, si ine mbali ya thupi,” zimenezo sizingapangitse kuti phazilo lisakhale mbali ya thupi.
16 Ndipo ngati khutu linganene kuti: “Popeza si ine diso, si ine mbali ya thupi,” zimenezo sizingapangitse kuti khutulo lisakhale mbali ya thupi.
17 Thupi lonse likanakhala diso, kodi bwenzi tikumva ndi chiyani? Nanga thupi lonse likanakhala khutu, kodi bwenzi tikumanunkhiza ndi chiyani?
18 Koma Mulungu anaika ziwalo zonse za thupi, chilichonse pamalo ake, mmene iye anafunira.
19 Ziwalo zonse zikanakhala chiwalo chimodzi, kodi thupi likanakhalapo?
20 Choncho pali ziwalo zambiri, koma thupi ndi limodzi.
21 Diso silingauze dzanja kuti: “Ndilibe nawe ntchito,” kapenanso, mutu sungauze mapazi kuti: “Ndilibe nanu ntchito.”
22 Ndipotu ziwalo zimene zimaoneka ngati zofooka, ndi zofunika.
23 Ndipo ziwalo zimene timaziona ngati zonyozeka, nʼzimene timazipatsa ulemu wambiri.+ Choncho ziwalo za thupi lathu zosaoneka bwino ndi zimene timazisamalira kwambiri,
24 Koma ziwalo zathu zooneka bwino kale sizifunikira kuzisamalira choncho. Komabe Mulungu analumikiza bwino thupi lonse, kuti ziwalo zomwe zilibe ulemu wokwanira zizisamaliridwa kwambiri.
25 Anachita zimenezi kuti thupi lisakhale logawanika, koma ziwalo zake zizisamalirana.+
26 Ndipo chiwalo chimodzi chikavutika, ziwalo zina zonse zimavutika nacho limodzi,+ komanso chiwalo china chikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalala nacho limodzi.+
27 Ndinu thupi la Khristu+ ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.+
28 Mulungu wapereka zochita kwa munthu aliyense mumpingo. Choyamba atumwi,+ chachiwiri aneneri,+ chachitatu aphunzitsi,+ kenako ntchito zamphamvu,+ mphatso zochiritsa,+ utumiki wothandiza anthu, luso loyendetsa zinthu+ ndiponso mphatso zolankhula zilankhulo zosiyanasiyana.*+
29 Sikuti onse angakhale atumwi. Ndipo sizingatheke kuti onse akhale aneneri. Kodi onse angakhale aphunzitsi? Nanga onse angamachite ntchito zamphamvu?
30 Komanso si onse amene ali ndi mphatso zochiritsa. Si onse amene amalankhula zilankhulo zosiyanasiyana.*+ Ndiponso onse sangakhale omasulira.+
31 Choncho yesetsani kuti mulandire mphatso zazikulu.+ Komabe, ndikuonetsani njira yopambana.+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “pamene munali anthu a mitundu ina.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malilime.”
^ Kapena kuti, “tinamwetsedwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malilime.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malilime.”