Yesaya 6:1-13
6 M’chaka chimene Mfumu Uziya inamwalira,+ ine ndinaona Yehova+ atakhala pampando wachifumu+ wolemekezeka umene unali pamalo okwezeka, ndipo zovala zake zinadzaza m’kachisi.+
2 Pamwamba pake panali aserafi.+ Mserafi aliyense anali ndi mapiko 6. Mapiko awiri anaphimbira nkhope yake,+ awiri anaphimbira mapazi ake ndipo awiri anali kuulukira.
3 Aliyense anali kuuza mnzake kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu.+ Zonse zimene zili padziko lapansi zimasonyeza ulemerero wake.”
4 Chifukwa cha mawuwo, mafelemu a zitseko+ anayamba kunjenjemera ndipo pang’ono ndi pang’ono, m’nyumbamo munadzaza utsi.+
5 Ine ndinati: “Tsoka kwa ine! Popeza maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.+ Nditsikira kuli chete pakuti ndine munthu wa milomo yodetsedwa,+ ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.”+
6 Pamenepo mserafi mmodzi anaulukira kwa ine. M’manja mwake munali khala lamoto+ limene analitenga paguwa lansembe ndi chopanira.+
7 Iye anakhudza pakamwa panga+ n’kunena kuti: “Taona! Khalali lakhudza milomo yako, chotero zolakwa zako zachoka ndipo machimo ako aphimbidwa.”+
8 Kenako ndinayamba kumva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?”+ Ine ndinayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”+
9 Iye anapitiriza kunena kuti: “Pita ukauze anthu awa kuti, ‘Imvani mobwerezabwereza anthu inu, koma musamvetsetse. Onani mobwerezabwereza, koma musazindikire chilichonse.’+
10 Ukachititse anthu awa kuumitsa mtima wawo,+ ndipo ukachititse makutu awo kuti asamamve.+ Ukamate maso awo kuti asamaone ndi maso awowo, ndiponso kuti asamamve ndi makutu awo, komanso kuti mtima wawo usamvetsetse zinthu, kuti angatembenuke n’kuchira.”+
11 Pamenepo ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, Yehova?”+ Iye anayankha kuti: “Mpaka mizinda yawo itawonongedwa n’kukhala bwinja, yopanda wokhalamo. Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo, ndiponso mpaka nthaka itawonongekeratu.+
12 Mpaka Yehova atathamangitsira anthu kutali, ndiponso mpaka mbali yaikulu ya dzikolo itakhala bwinja.+
13 M’dzikolo mudzakhalabe chakhumi+ ndipo chidzakhalanso chinthu chofunika kuchitentha ngati mtengo waukulu, ndiponso ngati chimtengo chachikulu, chimene chikadulidwa+ pamatsala chitsa.+ Mbewu yopatulika idzakhala chitsa chake.”+