Yesaya 53:1-12
53 Kodi ndani wakhulupirira zimene ife tamva?+ Ndipo kodi dzanja la Yehova+ laonetsedwa kwa ndani?+
2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pa winawake, ndiponso ngati muzu m’dziko lopanda madzi. Alibe maonekedwe alionse apamwamba kapena okongola,+ ndipo maonekedwe ake si osiririka m’maso mwathu.+
3 Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa.+ Anali munthu amene anadziwa kupweteka ndiponso amene anadziwa matenda.+ Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake.+ Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.+
4 Zoonadi, iye anatinyamulira matenda athu+ ndipo anatisenzera zowawa zathu.+ Koma ifeyo tinamuona ngati wosautsidwa,+ wokwapulidwa ndi Mulungu,+ ndiponso wozunzidwa.+
5 Iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+ Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+ Chilango chotibweretsera mtendere chinam’gwera iyeyo,+ ndipo chifukwa cha zilonda zake+ ifeyo tachiritsidwa.+
6 Tonsefe tinkangoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa.+ Aliyense analowera njira yake ndipo Yehova wachititsa cholakwa cha aliyense wa ife kugwera pa ameneyo.+
7 Iye anapanikizidwa+ ndipo analola kuti asautsidwe,+ koma sanatsegule pakamwa pake. Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa,+ ndipo mofanana ndi nkhosa yaikazi imene imakhala chete akamaimeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.+
8 Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.+ Ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo ake?+ Pakuti iye anadulidwa+ m’dziko la amoyo.+ Chifukwa cha zolakwa+ za anthu anga, iye anakwapulidwa.+
9 Manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa,+ ndipo adzakhala limodzi ndi anthu olemera pa imfa yake,+ ngakhale kuti iye sanachite zachiwawa zilizonse+ ndipo m’kamwa mwake munalibe chinyengo.+
10 Koma zinamukomera Yehova kuti mtumiki wake aphwanyidwe.+ Iye anamulola kuti adwale.+ Mukapereka moyo wake monga nsembe ya kupalamula,+ iye adzaona ana ake.+ Adzatalikitsa masiku ake+ ndipo ndi dzanja lake, adzakwaniritsa zokonda+ Yehova.+
11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino+ ndipo adzakhutira.+ Chifukwa cha zimene akudziwa, mtumiki wanga wolungamayo+ adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+ ndipo adzasenza zolakwa zawo.+
12 Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri+ ndipo iye adzagawana zolanda ndi amphamvu,+ chifukwa anakhuthula moyo wake mu imfa+ ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa.+ Iye ananyamula tchimo la anthu ambiri+ ndipo analowererapo kuti athandize olakwa.+