Yesaya 5:1-30
5 Ndikufuna ndimuimbire nyimbo munthu amene ndimamukonda. Imeneyi ndi nyimbo yonena za munthu amene ndimamukonda, ndiponso munda wake wa mpesa.+ Wokondedwa wanga anali ndi munda wa mpesa pamalo achonde m’mbali mwa phiri.
2 Iye analima mundawo n’kuchotsamo miyala, kenako anabzalamo mphesa zofiira zabwino kwambiri. Anamanga nsanja pakati pa mundawo.+ Anasemamonso choponderamo mphesa.+ Iye anali kuyembekezera kuti mundawo ubereka mphesa zabwino,+ koma unabereka mphesa zam’tchire.+
3 “Tsopano inu anthu okhala mu Yerusalemu ndiponso inu amuna a mu Yuda, weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesa.+
4 N’chiyaninso chimene ndingachite m’munda wanga wa mpesawu chimene sindinachitemo kale?+ Ine ndinali kuyembekezera kuti ubereka mphesa zabwino, koma n’chifukwa chiyani unabereka mphesa zam’tchire?
5 Tsopano amuna inu, ndikuuzani zimene ndichite ndi munda wanga wa mpesa: Ndichotsa zomera zimene zinali ngati mpanda wa mundawo,+ ndipo ndiutentha.+ Ndigumula mpanda wake wamiyala ndipo mundawo udzangokhala malo oti azipondapondapo.+
6 Ndidzangousiya kuti uwonongeke.+ Sindidzatengulira mitengo yake ndipo sindidzaulimanso.+ M’mundamo mudzamera tchire ndi zitsamba zaminga,+ ndipo ndidzalamula mitambo kuti isagwetsere mvula pamundawo.+
7 Ine ndine Yehova wa makamu ndipo Isiraeli ndi munda wanga wa mpesa.+ Amuna a ku Yuda ndiwo mitengo ya mpesa imene ndinali kuikonda.+ Ine ndinali kuyembekezera chilungamo+ koma ndinaona anthu akuphwanya malamulo. Ndinali kuyembekezera zolungama koma ndinaona anthu akulira.”+
8 Tsoka kwa anthu amene akuwonjezera nyumba zina panyumba zawo,+ ndiponso amene akuwonjezera minda ina kuminda yawo, mpaka malo onse kutha,+ ndipo amuna inu mwayamba kukhala nokhanokha m’dzikoli.
9 Ndamva Yehova wa makamu akulumbira kuti nyumba zambiri, ngakhale zitakhala zikuluzikulu ndiponso zabwino, zidzakhala chinthu chodabwitsa kwambiri ndipo zidzakhala zopanda wokhalamo.+
10 Pakuti maekala 10*+ a munda wa mpesa adzatulutsa mtsuko*+ umodzi wokha wa vinyo, ndipo mbewu zokwana muyezo umodzi wa homeri* zidzatulutsa zokolola zokwana muyezo umodzi wokha wa efa.*+
11 Tsoka kwa anthu amene amadzuka m’mawa kuti akafunefune chakumwa choledzeretsa.+ Amene amakhala akumwabe mpaka madzulo kutada, moti vinyo amawaledzeretsa.+
12 Pa zikondwerero zawo amaimbapo azeze, zoimbira za zingwe, maseche, ndi zitoliro ndipo amamwapo vinyo.+ Koma sayang’ana ntchito ya Yehova, ndipo ntchito ya manja ake saiona.+
13 Chotero anthu anga adzapita ku ukapolo kudziko lina chifukwa chosadziwa zinthu.+ Anthu awo olemekezeka adzakhala amuna anjala+ ndipo khamu lawo lidzakhala louma kukhosi ndi ludzu.+
14 Choncho, Manda* akulitsa malo ake ndipo atsegula kwambiri pakamwa pake kupitirira malire.+ Anthu olemekezeka a mumzindawo, khamu lake, phokoso lake ndi chikondwerero chake zidzatsikira m’mandamo.+
15 Munthu wochokera kufumbi adzawerama. Iye adzatsika, ndipo ngakhale maso a anthu okwezeka adzatsika.+
16 Yehova wa makamu adzakwezeka kudzera m’chiweruzo,+ ndipo Mulungu woona, Woyera,+ adzadziyeretsa kudzera m’chilungamo.+
17 Kumeneko, ana a nkhosa amphongo adzadyako msipu ngati kuti ali pamalo odyetserapo ziweto. M’mabwinja mmene kale munali nyama zodyetsedwa bwino, alendo adzadyeramo.+
18 Tsoka kwa amene amakoka zolakwa ndi zingwe zopanda choonadi, ndi amene amakoka machimo ngati akuwakoka ndi zingwe zokokera ngolo.+
19 Tsoka kwa amene amanena kuti: “Ntchito yake ifulumire, ibwere mwamsanga kuti tiione. Cholinga cha Woyera wa Isiraeli chichitike kuti tichidziwe.”+
20 Tsoka kwa amene akunena kuti chabwino n’choipa ndipo choipa n’chabwino,+ amene akuika mdima m’malo mwa kuwala ndi kuwala m’malo mwa mdima, amene akuika zowawa m’malo mwa zotsekemera,* ndi zotsekemera m’malo mwa zowawa.+
21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru komanso amadziyesa ochenjera.+
22 Tsoka kwa anthu amene ali eni ake omwa vinyo kwambiri, ndi kwa anthu amene ali akatswiri odziwa kusakaniza zakumwa zoledzeretsa.+
23 Tsoka kwa anthu amene amanena kuti woipa ndi wolungama chifukwa cholandira chiphuphu,+ ndiponso kwa amene amanena kuti wolungama ndi wolakwa.+
24 Chotero monga momwe lawi la moto limanyeketsera mapesi+ komanso monga mmene udzu wouma umanyekera m’malawi a moto, muzu wawo udzawola n’kuyamba kununkha.+ Maluwa awo adzauma n’kuuluzika ngati fumbi, chifukwa akana malamulo a Yehova wa makamu+ ndipo anyoza mawu a Woyera wa Isiraeli.+
25 N’chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake ndipo adzatambasula dzanja lake n’kuwapha.+ Mapiri adzanjenjemera+ ndipo mitembo yawo idzakhala ngati zinyalala m’misewu.+
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.
26 Iye waikira chizindikiro mtundu waukulu wakutali.+ Wauimbira likhweru kumapeto kwa dziko lapansi.+ Ndipotu mtunduwo udzachita changu n’kubwera msangamsanga.+
27 Pakati pawo palibe aliyense wotopa ndipo palibe amene akupunthwa. Palibe amene akuwodzera ndipo palibe amene akugona. Lamba wa m’chiuno mwawo sadzamasulidwa ndipo zingwe za nsapato zawo sizidzaduka.
28 Mivi yawo ndi yakuthwa ndipo mauta awo onse ndi okungika.+ Ziboda za mahatchi awo n’zolimba ngati mwala wa nsangalabwi.+ Mawilo a magaleta awo ali ngati mphepo yamkuntho.+
29 Kubangula kwawo kuli ngati kwa mkango ndipo amabangula ngati mikango yamphamvu.+ Iwo adzabangula n’kugwira nyama. Adzainyamula bwinobwino ndipo sipadzakhala woipulumutsa.+
30 Iwo adzabangulira nyamayo m’tsiku limenelo ngati mkokomo wa nyanja.+ Munthu adzayang’ana dzikolo n’kuona kuti muli mdima womvetsa chisoni.+ Ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mvula imene idzagwe m’dzikolo.
Mawu a M'munsi
^ Zikuoneka kuti amenewa anali malo aakulu pafupifupi mahekitala anayi.
^ Onani Zakumapeto 12.
^ Onani Zakumapeto 12.
^ Muyezo umodzi wa efa ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
^ Onani Zakumapeto 5.
^ Ena amati “zonzuna.”