Yesaya 32:1-20

32  Taonani! Mfumu+ idzalamulira mwachilungamo,+ ndipo akalonga+ adzalamuliranso mwachilungamo.  Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho,+ ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi,+ ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.+  Maso a anthu otha kuona sadzatsekeka, ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsera mwatcheru.+  Mtima wa anthu opupuluma udzafunafuna kudziwa zinthu,+ ndipo ngakhale lilime la anthu achibwibwi lidzalankhula bwinobwino zinthu zomveka.+  Munthu wopusa sadzatchedwanso wopatsa, ndipo munthu wopanda khalidwe sadzatchedwa wolemekezeka,+  pakuti munthu wopusa adzalankhula zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mtima wake udzaganiza zochita zinthu zopweteka ena.+ Iye adzachita zimenezi kuti azichita zopanduka,+ kuti azinenera Yehova zoipa, kuti achititse mimba ya munthu wanjala kukhala yopanda kanthu,+ ndiponso kuti achititse munthu waludzu kukhala wopanda chilichonse choti amwe.  Munthu wakhalidwe loipayo, njira zake n’zoipa.+ Iye amakonza zochita khalidwe lotayirira,+ n’cholinga choti apweteke anthu ozunzika pogwiritsa ntchito mawu abodza,+ ngakhale pamene munthu wosauka akunena zoona.  Koma munthu wopatsa amapereka malangizo okhudza kupatsa, ndipo iyeyo amapitiriza kukhala wopatsa.+  “Inu akazi amene mukukhala mosatekeseka, nyamukani! Mvetserani mawu anga!+ Inu ana aakazi osasamala, mverani zimene ndikunena! 10  Pomatha chaka ndi masiku angapo, anthu osasamalanu mudzatekeseka,+ chifukwa ngakhale nyengo yokolola mphesa itatha, sipadzakhala mphesa zilizonse zimene zasonkhanitsidwa.+ 11  Inu akazi amene mukukhala mosatekeseka, njenjemerani! Inu osasamala, chitani mantha! Vulani n’kukhala maliseche, ndipo muvale ziguduli m’chiuno mwanu.+ 12  Dzimenyeni pachifuwa pomva chisoni+ chifukwa cha kuwonongeka kwa minda yachonde+ ndi minda ya mpesa. 13  Panthaka ya anthu anga, pakungomera zitsamba zaminga.+ Zamera panyumba zonse zimene kale zinali zodzaza ndi chisangalalo. Zamera m’tauni imene kale inali yodzaza ndi chikondwerero.+ 14  Pakuti nsanja yokhalamo yasiyidwa,+ piringupiringu amene anali mumzindamo watha. Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka tchire. Mpaka kalekale zidzakhala malo osangalalako mbidzi, ndi odyetserako ziweto, 15  kufikira mzimu utatsanulidwa pa ife kuchokera kumwamba,+ ndiponso chipululu chitakhala munda wa zipatso. Munda wa zipatsowo udzakhala ngati nkhalango yeniyeni.+ 16  “M’chipululumo mudzakhala chilungamo, ndiponso m’munda wa zipatsowo mudzakhala chilungamo.+ 17  Ntchito ya chilungamo chenicheni idzakhala mtendere,+ ndipo zochita za chilungamo chenicheni zidzakhala bata ndi mtendere mpaka kalekale.+ 18  Anthu anga adzakhala pamalo amtendere ndi pamalo otetezeka. Adzakhala m’malo abata ndiponso aphee!+ 19  Kudzagwa matalala nkhalango ikadzatha,+ ndiponso mzinda ukadzatsitsidwa n’kukhala wonyozeka.+ 20  “Odala ndinu anthu amene mukubzala mbewu m’mphepete mwa madzi onse,+ ndi kumasula ng’ombe yamphongo ndi bulu.”+

Mawu a M'munsi