Yeremiya 47:1-7

47  Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza Afilisiti.+ Pa nthawiyi, Farao anali asanathire nkhondo mzinda wa Gaza.+  Yehova anati: “Taonani! Madzi akubwera+ kuchokera kumpoto+ ndipo madzi ake ndi achigumula. Adzamiza dziko ndi zonse zokhala mmenemo.+ Adzamizanso mzinda ndi zonse zokhala mmenemo. Amuna adzalira mokuwa, ndipo aliyense wokhala m’dzikolo adzalira mofuula.+  Abambo adzathawa osayang’ana m’mbuyo kuti apulumutse ana awo. Adzachita izi chifukwa chakuti sadzalimba mtima pakumva mgugu wa mahatchi ake,+ phokoso la magaleta ake ankhondo+ ndi kulira kwa mawilo ake.+  Iwo adzachita mantha chifukwa cha tsiku limene likubwera. Tsikuli ndi lofunkha zinthu za Afilisiti+ onse ndi kupha wopulumuka aliyense wothandiza+ Turo+ ndi Sidoni.+ Pakuti Yehova adzafunkha zinthu za Afilisiti+ amene atsala ochokera pachilumba cha Kafitori.+  Gaza+ adzameta mpala+ chifukwa cha chisoni. Asikeloni+ amuwononga ndi kumukhalitsa chete. Inu otsala a m’chigwa cha Gaza ndi Asikeloni, mudzadzichekacheka kufikira liti?+  “Eyaa! iwe lupanga la Yehova.+ Kodi sukhala chete kufikira liti? Bwerera m’chimake.+ Pumula, ndipo ukhale chete.  “Kodi lupangali lingakhale chete bwanji pamene Yehova ndi amene walilamula? Liyenera kupita ku Asikeloni ndi m’mphepete mwa nyanja.+ Iye walituma kuti likakhale kumeneko.”

Mawu a M'munsi