Yeremiya 41:1-18

41  Tsopano m’mwezi wa 7, Isimaeli+ mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama,+ anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa+ pamodzi ndi amuna ena 10.+ Isimaeli anali wa m’banja lachifumu+ ndipo analinso mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. Atafika kumeneko anayamba kudya chakudya pamodzi.+  Ndiyeno Isimaeli mwana wa Netaniya ndi amuna 10 amene anali naye ananyamuka ndi kukapha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani. Choncho Isimaeli anapha munthu amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira dzikolo.+  Isimaeli anaphanso Ayuda onse amene anali ndi Gedaliya ku Mizipa pamodzi ndi Akasidi, amuna ankhondo, amene anawapeza kumeneko.  Pa tsiku lachiwiri kuchokera pamene Gedaliya anaphedwa, munthu aliyense asanadziwe zimenezi,+  kunabwera amuna ochokera ku Sekemu,+ ku Silo+ ndi ku Samariya.+ Iwo analipo 80 ndipo anabwera atameta ndevu,+ atadzichekacheka ndiponso atang’amba zovala zawo.+ Amunawa anabwera ndi nsembe yambewu ndi lubani+ m’manja mwawo kuti adzazipereke kunyumba ya Yehova.  Ndiyeno Isimaeli mwana wa Netaniya ananyamuka ku Mizipa akulira kuti akakumane nawo.+ Atakumana nawo anawauza kuti: “Tiyeni kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu.”  Koma anthuwo atafika pakati pa mzinda, Isimaeli mwana wa Netaniya anawapha ndi kuwaponya m’chitsime. Iye anapha anthuwa mothandizana ndi amuna amene anali naye.+  Tsopano pakati pa anthuwo panali amuna 10 amene anauza Isimaeli mofulumira kuti: “Usatiphe, pakuti tili ndi chuma chobisika m’munda. Tili ndi tirigu, barele, mafuta ndi uchi.”+ Chotero Isimaeli anawasiya ndipo sanawaphe mmene anachitira ndi abale awo.  Chitsime chimene Isimaeli+ anaponyamo mitembo yonse ya amuna amene anawapha chinali chachikulu kwambiri. Mfumu Asa ndi imene inakumba chitsime chimenechi pamene Basa mfumu ya Isiraeli inamuopseza.+ Chitsime chimenechi ndi chimene Isimaeli mwana wa Netaniya anaponyamo mitembo ya anthu amene anawapha. 10  Kenako Isimaeli anagwira anthu onse otsala, ana aakazi a mfumu,+ amene anali ku Mizipa.+ Anagwiranso anthu ena onse otsala ku Mizipa+ amene Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawapereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu+ kuti aziwayang’anira. Chotero Isimaeli mwana wa Netaniya anawagwira ndipo ananyamuka kuti awolokere nawo kudziko la ana a Amoni.+ 11  Patapita nthawi, Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo+ amene anali naye anamva zoipa zonse zimene Isimaeli mwana wa Netaniya anachita. 12  Choncho iwo anatenga amuna onse ndi kupita kukamenyana ndi Isimaeli mwana wa Netaniya. Iwo anamupeza pafupi ndi madzi ambiri a ku Gibeoni.+ 13  Ndiyeno anthu onse amene anali ndi Isimaeli ataona Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali naye, anayamba kusangalala kwambiri. 14  Anthu onse amene Isimaeli anawagwira ku Mizipa+ anatembenuka ndi kuthawira kwa Yohanani mwana wa Kareya. 15  Koma Isimaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi amuna 8 anathawa+ ataona Yohanani. Iye anathawira kwa ana a Amoni. 16  Ndiyeno Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali naye anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa. Anthu amenewa anawalanditsa m’manja mwa Isimaeli mwana wa Netaniya amene anawagwira atapha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu. Analanditsa amuna amphamvu, amuna ankhondo, akazi awo, ana ndi nduna za panyumba ya mfumu. Yohanani analanditsa anthu amenewa ku Gibeoni. 17  Iwo anakakhala kumalo ogona a Chimamu pafupi ndi Betelehemu+ ndi cholinga choti apitirize ulendo wawo kukalowa mu Iguputo.+ 18  Anachita zimenezi chifukwa cha Akasidi.+ Iwo anali kuopa Akasidiwo+ chifukwa chakuti Isimaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu+ amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira dzikolo.+

Mawu a M'munsi