Yeremiya 39:1-18
39 M’chaka cha 9 cha ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 10,+ Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anafika ku Yerusalemu ndi kuzungulira mzindawo.+
2 M’chaka cha 11 cha ulamuliro wa Zedekiya, m’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9, anaboola mpanda wa mzindawo.+
3 Ndiyeno akalonga onse a mfumu ya Babulo analowa mumzindamo ndi kukhala pansi ku Chipata cha Pakati.+ Mayina a akalongawo anali Nerigali-sarezera, Samugari-nebo, Sarisekimu, Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akalonga ena onse a mfumu ya Babulo.
4 Ndiyeno Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse ankhondo ataona adaniwo anayamba kuthawira+ kunja kwa mzinda usiku. Iwo analowera njira ya kumunda wa mfumu,+ kukatulukira pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, n’kupitiriza kuthawa molowera ku Araba.+
5 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+
6 Zitatero mfumu ya Babulo inapha+ ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, Zedekiyayo akuona.+ Inaphanso akuluakulu onse a ku Yuda.+
7 Mfumu ya Babulo inachititsa khungu maso a Zedekiya+ ndipo kenako inamumanga m’maunyolo amkuwa kuti apite naye ku Babulo.
8 Akasidi anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu onse.+ Iwo anagwetsanso mpanda wa Yerusalemu.+
9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+
10 Ndiyeno ena mwa anthuwo, anthu onyozeka amene analibe kalikonse, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawasiya m’dziko la Yuda,+ ndipo pa tsiku limenelo anawapatsa minda ya mpesa ndi ntchito zokakamiza kuti azigwira.+
11 Kuwonjezera pamenepo, Nebukadirezara mfumu ya Babulo anapereka lamulo lokhudza Yeremiya kwa Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, kuti:
12 “Mtenge uzimuyang’anira ndipo usamuchitire choipa chilichonse.+ Koma uzimuchitira chilichonse chimene iye wanena.”+
13 Pamenepo Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu pamodzi ndi Nebusazibani amene anali Rabisarisi, Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi ndi akuluakulu onse a mfumu ya Babulo anatuma anthu.
14 Iwo anatuma anthuwo kuti akatenge Yeremiya m’Bwalo la Alonda+ ndi kumupereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ kuti apite naye kunyumba kwake, kuti Yeremiyayo akakhale pakati pa anthu akwawo.
15 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yeremiya pamene anali wotsekeredwa m’Bwalo la Alonda.+ Iye anamuuza kuti:
16 “Pita kwa Ebedi-meleki+ Mwitiyopiya ukamuuze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Taona! Ndikukwaniritsa mawu anga akuti mzinda uwu ndiugwetsera tsoka osati zinthu zabwino.+ Pa tsikulo zimene ndinanena zidzachitika iwe ukuona.”’+
17 “‘Pa tsikulo ndidzakulanditsa+ ndipo sudzaperekedwa m’manja mwa anthu amene umawaopa,’+ watero Yehova.
18 “‘Pakuti ine ndidzakupulumutsa ndithu, ndipo sudzaphedwa ndi lupanga, koma udzapulumutsa moyo wako+ chifukwa chakuti wandikhulupirira,’+ watero Yehova.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “mkulu wa nduna za panyumba ya mfumu.”
^ Kapena kuti “mkulu wa azamatsenga (wolosera zam’tsogolo, wopenda nyenyezi), mkulu wa akuluakulu.”