Yeremiya 20:1-18
20 Tsopano Pasuri, mwana wa Imeri,+ wansembe, amenenso anali mtumiki wamkulu panyumba ya Yehova,+ anakhala tcheru kumvetsera pamene Yeremiya anali kulosera mwa kunena mawu amenewa.
2 Kenako Pasuri anamenya mneneri Yeremiya+ ndi kumuika m’matangadza+ amene anali pa Chipata Chakumtunda cha Benjamini, cha m’nyumba ya Yehova.
3 Ndiyeno pa tsiku lotsatira, Pasuri anamasula Yeremiya m’matangadzawo.+ Pamenepo Yeremiya anamuuza kuti:
“Yehova wanena kuti dzina lako+ silikhalanso Pasuri koma Chochititsa Mantha paliponse.+
4 Pakuti Yehova wanena kuti, ‘Inetu ndikukusandutsa chinthu chochititsa mantha kwa iwe mwini ndi kwa anzako onse, ndipo adzaphedwa ndi lupanga la adani awo+ iwe ukuona.+ Anthu onse a mu Yuda ndidzawapereka m’manja mwa mfumu ya ku Babulo. Ena adzapita nawo ku Babulo ndipo ena adzawapha ndi lupanga.+
5 Ndipo ndidzatenga zinthu zonse zosungidwa mumzindawu, katundu wawo yense, zinthu zonse zamtengo wapatali ndi chuma chonse cha mafumu a Yuda, n’kuzipereka m’manja mwa adani awo.+ Ndipo adaniwo adzafunkha zinthu zimenezi ndi kupita nazo ku Babulo.+
6 Koma kunena za iwe Pasuri, ndi onse okhala m’nyumba yako, mudzapita ku ukapolo.+ Iwe udzapita ku Babulo ndipo udzafera kumeneko ndi kuikidwa m’manda komweko pamodzi ndi anzako onse,+ chifukwa walosera kwa iwo monama.’”+
7 Mwandidabwitsa inu Yehova, ndipo ndadabwa. Mwagwiritsa ntchito mphamvu zanu pa ine ndipo mwapambana.+ Ndakhala chinthu choseketsa tsiku lonse. Aliyense akungondinyoza.+
8 Nthawi zonse ndikalankhula mawu anu ndimalira. Ndimanena za chiwawa ndi kufunkhidwa,+ pakuti mawu a Yehova achititsa kuti ndizinyozedwa ndi kutonzedwa tsiku lonse.+
9 Choncho ndinanena kuti: “Sindidzanenanso za iye ndipo sindidzalankhulanso m’dzina lake.”+ Koma mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka. Anali ngati moto woyaka umene autsekera m’mafupa anga. Choncho ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule moti sindinathenso kupirira.+
10 Pakuti ndinamva zoipa zimene ambiri anali kunena.+ Zinali zochititsa mantha paliponse. Iwo anali kunena kuti, “Fotokozani kuti ifenso tinene za iye.”+ Munthu aliyense anali kundiuza kuti “Mtendere!” koma anali kundiyang’anira kuti ndilakwitse chinachake+ ndipo anali kunena kuti: “Achita chinachake chopusa+ ameneyu ndipo timugonjetsa ndi kumubwezera.”
11 Koma Yehova anali nane+ ngati msilikali wamphamvu ndi woopsa.+ N’chifukwa chake anthu amene akundizunza adzakhumudwa ndipo sadzapambana.+ Adzachita manyazi kwambiri chifukwa adzaona kuti sizinawayendere bwino. Manyazi awo adzakhala nawo mpaka kalekale ndipo sadzaiwalika.+
12 Inu Yehova wa makamu, mumasanthula munthu wolungama.+ Mumaona impso ndi mtima wake.+ Ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango,+ pakuti ine ndakufotokozerani mlandu wanga.+
13 Imbirani Yehova anthu inu! Tamandani Yehova! Pakuti walanditsa moyo wa munthu wosauka m’manja mwa anthu ochita zoipa.+
14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa! Tsiku limene mayi anga anandibereka lisadalitsike!+
15 Atembereredwe munthu amene anabweretsa uthenga wabwino kwa bambo anga powauza kuti: “Mkazi wako wakuberekera mwana wamwamuna.” Munthuyo anawasangalatsa kwambiri bambo anga.+
16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova waigonjetsa popanda kuimvera chisoni.+ M’mawa kwambiri azimva kulira kofuula ndipo masana azimva chizindikiro chochenjeza.+
17 N’chifukwa chiyani sanandiphe ndili m’mimba kuti mayi anga akhale manda anga, ndiponso kuti akhale ndi pakati mpaka kalekale?+
18 N’chifukwa chiyani ndinabadwa?+ Kodi ndinabadwa kuti ndidzagwire ntchito yakalavulagaga ndi kukhala wachisoni,+ ndi kuti moyo wanga ufike kumapeto kwake ndili wamanyazi?+